Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuteteza Zachilengedwe ku Warwick

Kuteteza Zachilengedwe ku Warwick

A Mboni za Yehova ayamba ntchito yomanga maofesi omwe akhale likulu lawo latsopano la padziko lonse pafupi ndi nyanja ina imene ili m’dera la nkhalango. Nyanjayi imatchedwa Sterling Forest (kapena kuti nyanja ya Blue) ndipo ili m’dera la kumidzi m’chigawo cha New York. Kodi a Mboniwa akuchita zotani pofuna kuteteza nyama zakutchire komanso nkhalangoyo?

A Mboniwo anamanga mpanda wongoyembekezera kuzungulira malo onse amene akugwirapo ntchito yomangayo. Cholinga cha mpandawo ndi kuteteza nyama, monga njoka ndi akamba, kuti zisalowe kumalo a ntchitowo chifukwa zingavulazidwe. Mpandawu umayenderedwa nthawi ndi nthawi pofuna kutsimikiza kuti nyama sizingalowe kumalo a ntchitowo. Ntchito yomangayi ikadzatha, mpandawu udzachotsedwa ndipo njoka iliyonse imene ingapezeke pafupi ndi maofesiwa, izitengedwa ndi munthu wophunzitsidwa bwino n’kukaibwezeretsa kunkhalango.

Kambalame kokongola

Mitengo yomwe inafunika kudulidwa inadulidwa m’nyengo yozizira popewa kusokoneza mbalame zomwe zimamanga zisa zawo m’mitengoyo n’kumaswana munyengo yotentha. Ntchito yomangayi ikadzatha, a Mboniwo adzaika zikwere m’malo amene adula mitengo n’cholinga choti mbalame zija zipeze malo oswanirana.

Komanso a Mboni za Yehovawo anasankha kuti ntchito yolambula ndi kukumba m’malo osiyanasiyana, ichitike kuyambira m’mwezi wa October mpaka March. Cholinga cha zimenezi n’chakuti njere za maluwa enaake osowa kwambiri zimwazikane n’kumera bwinobwino. Iwo akuyesetsa kuchita zimenezi ngakhale kuti maluwa a mtundu umenewu sanapezekepo pamalopa kuyambira pamene ntchito yomangayi inayamba mu 2007.

Ntchito yomangayi ikuchitika m’mbali mwenimweni mwa nyanja ya Sterling Forest, ndipo m’nyanjayi muli nsomba za mitundu yosiyanasiyana. Komanso mbalame zamitundu yambirimbiri zimapezeka kunyanjayi. Pofuna kuteteza nyanjayi, akatswiri okonza mapulani a zomangamanga, akonza zoti ntchito yonse yomanga ikadzatha, pamalopo pazioneka pa girini. Mwachitsanzo, madenga onse a nyumba za pamalowa adzawakonza m’njira yoti pamwamba pake adzadzalepo zinthu monga kapinga ndi maluwa. Zimenezi zidzathandiza kuteteza chilengedwe komanso zidzathandiza kuti nthaka isamakokoloke ndi madzi a mvula ochokera padenga. Kowonjezera pamenepa, mitengo ndi zomera zonse zimene zili m’mbali mwa nyanjayi zikutetezeredwa.

Munthu wina wa Mboni amene akugwira nawo ntchitoyi anati: “Ngakhale kuti zonse zimene tasankha kuchitazi n’zofuna nthawi yambiri komanso kukonza bwino mapulani, taona kuti ndi bwino kuchita zimenezi n’cholinga choti tisawononge chilengedwe ku Warwick.”