Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Ntchito Yomasulira Msonkhano Wachigawo wa 2020 Wakuti ‘Kondwerani Nthawi Zonse.’

Ntchito Yomasulira Msonkhano Wachigawo wa 2020 Wakuti ‘Kondwerani Nthawi Zonse.’

JULY 10, 2020

 Kwa nthawi yoyamba m’mwezi wa July ndi August 2020, abale ndi alongo padziko lonse adzaonera msonkhano wachigawo pa nthawi imodzi. Kuti zimenezi zitheke, msonkhanowu unkafunika kumasuliridwa m’zinenero zoposa 500. Nthawi zambiri ntchito ngati imeneyi imatenga chaka kapena kuposerapo kuti imalizidwe. Koma malinga ndi mmene zinthu zilili chifukwa cha mliri wa Kolonavairasi, omasulira msonkhano wachigawo wa 2020 wakuti ‘Kondwerani Nthawi Zonse,’ anali ndi nthawi yosachepera miyezi 4 yokha kuti amalize ntchitoyi.

 A Dipatimenti Yothandiza Omasulira komanso Dipatimenti Yothandiza Kugula Zinthu kulikulu la padziko lonse la Mboni za Yehova, anathandiza kwambiri pa ntchito yaikulu imeneyi. A Dipatimenti Yothandiza Omasulira anaona kuti omasulira ambiri akufunika zipangizo zokwanira zowathandiza pa ntchitoyi, makamaka ma maikolofoni abwino. Choncho, a Dipatimenti Yothandiza Kugula Zinthu anakonza zogula ma maikolofoni okwana 1,000 kuti awatumize m’malo osiyanasiyana pafupifupi 200.

 Kuti tisawononge ndalama zambiri, tinagula ma maikolofoni ambiri n’kuwatumiza kumalo amodzi kenako n’kumawatumiza padziko lonse kumalo amene ankafunika. Chifukwa choti tinagula ma maikolofoni ambiri pa nthawi imodzi, maikolofoni iliyonse tinkaigula pamtengo wa madola 170. Mtengowu ukuphatikizapo ndalama zotumizira. Zimenezi zinathandiza kuti tiwagule motsika mtengo kusiyana ndi mmene zikanakhalira ngati tikanati tizigula imodziimodzi.

 A Dipatimenti Yothandiza Kugula Zinthu ankafunika kugula komanso kutumiza zinthuzi mu April ndi May 2020. Pa nthawiyi, mabizinezi ambiri sankayenda bwino chifukwa cha mliri wa Kolonavairasi. Komabe ngakhale zinali choncho, pofika kumapeto kwa May, zinthuzi zinali zitafika ku ma ofesi a nthambi ambiri komanso malo osiyanasiyana omasulira mabuku.

 M’bale Jay Swinney, woyang’anira m’Dipatimenti Yothandiza Kugula Zinthu ananena kuti: “Madipatimenti osiyanasiyana a pa Beteli ankachita zinthu mogwirizana kwambiri ndi anthu a bizinezi osiyanasiyana kuti ntchitoyi itheke. Mzimu wa Yehova ndi umene unathandiza kuti tichite zinthu mogwirizana chonchi, zomwe zinathandiza kuti ntchitoyi iyende mwachangu komanso kuti tithe kugwiritsa ntchito bwino ndalama zimene abale amapereka.”

 M’bale Nicholas Ahladis, yemwe amatumikira m’Dipatimenti Yothandiza Omasulira ananena kuti: “Omasulira, omwe pa nthawiyi sankagwirira ntchito pamalo amodzi, analimbikitsidwa kwambiri atalandira zipangizozi. Iwo ankatha kulumikizana n’kumamasulira komanso kujambula nkhani, masewero ndiponso nyimbo m’zinenero zoposa 500.”

 Ntchito yogula komanso kutumiza ma maikolofoniwa ndi imodzi mwa ntchito zomwe zinathandiza pokonza msonkhano wachigawo wa 2020, wakuti ‘Kondwerani Nthawi Zonse,’ womwe unakonzedwa kuti abale ndi alongo padziko lonse asangalale nawo. Zopereka zanu zimene mumapereka moolowa manja kudzera pa donate.pr418.com, komanso m’njira zina ndi zimene zinathandiza kuti tigulire zinthu zofunikazi.