Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

SEPTEMBER 12, 2014
GERMANY

Ku Sachsenhausen Kunachitika Mwambo Wokumbukira wa Mboni za Yehova Yemwe Anaphedwa ndi Chipani cha Nazi

Ku Sachsenhausen Kunachitika Mwambo Wokumbukira wa Mboni za Yehova Yemwe Anaphedwa ndi Chipani cha Nazi

SELTERS, Germany—Pa September 16, 2014, Bungwe lina loyang’anira malo osiyanasiyana okumbukira anthu amene anaphedwa kundende, (Brandenburg Memorials Foundation) linachita mwambo wokumbukira kuti patha zaka 75 kuchokera pamene a August Dickmann anaphedwa kundende ya Sachsenhausen. A Dickmann anali munthu woyamba kuphedwa ndi chipani cha Nazi chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Iwo anaphedwa pa nthawi ya Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse.

August Dickmann, m’ma 1936.

Mu October 1937, a Dickmann anaikidwa m’ndende ya Sachsenhausen, chifukwa cha zimene ankakhulupirira monga wa Mboni za Yehova. Kenako mu 1939, Nkhondo Yachiwiri ya Padziko Lonse inayamba. Patangodutsa masiku atatu chiyambireni nkhondoyi, gulu la Gestapo linalamula a Dickmann kuti asaine khadi la asilikali ndipo kungosaina khadili kukanachititsa kuti akhale m’gulu la asilikali a Chijeremani. Koma iwo anakana ndipo anaikidwa m’chipinda chaokha. Kenako mkulu wa ndende anapempha chilolezo kwa mkulu wa gulu lachitetezo la chipani cha Nazi, lomwe limatchedwa kuti SS, chakuti a Dickmann aphedwe pamaso pa anzawo onse omwe anali nawo limodzi kundendeko. Pa September 15, 1939, a Mboni za Yehova ambirimbiri kuphatikizapo a Heinrich, omwe ndi achimwene awo a Dickmann, anakakamizidwa kuti aonerere a Dickmann akuphedwa. Patapita masiku awiri, nyuzipepala ina inanena kuti: “A August Dickmann, a zaka 29, . . . aphedwa mochita kuwomberedwa ndi gulu lina la asilikali.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti a Dickmann anaphedwa chifukwa chokana kulowa usilikali “potsatira mfundo za m’chipembedzo chawo.”—The New York Times.

Pa September 18, 1999, chipilala chokumbukira a Mboni za Yehova oposa 890 omwe anali m’ndende ya Sachsenhausen chinaikidwa kunja kwa khoma la ndende yakale. Patsikuli anaikanso mwala wokumbukira malemu Dickmann.

Mwambowu unayambira pamene panaikidwa mwala wokumbukira a Dickmann. Kenako anakaupitirizira kumene kunali khitchini yakale ya akaidi komwe anthu osiyanasiyana analankhula. Dr. Detlef Garbe, woyang’anira malo akumbukira anthu omwe anazunzidwa kundende ya Neuengamme yemwenso amalemba mabuku, ndi amene analankhula monga mlendo wapadera pa mwambowu.

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Germany: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110