Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Dr. Gabriele Hammermann, mkulu wa malo osungirako mbiri yokhudza nkhanza zomwe zinkachitika pandende yozunzirako anthu ku Dachau, akulankhula pa mwambowu ndipo akusonyeza chikwangwani chofotokoza za a Max Eckert.

JULY 9, 2018
GERMANY

Mwambo Wokumbukira a Max Eckert Unachititsa Kuti Anthu Ambiri Awadziwe

Mwambo Wokumbukira a Max Eckert Unachititsa Kuti Anthu Ambiri Awadziwe

Pa mwambo womwe unachitika pa 7 May, 2018 pamalo osungirako mbiri yokhudza nkhanza zomwe zinkachitika pandende yozunzirako anthu ku Dachau, anthu 200 omwe anali pa mwambowu anasonyezedwa chikwangwani chofotokoza za M’bale Max Eckert. M’baleyu anamangidwa n’kuikidwa m’ndende ya ku Dachau momwe anakhalamo zaka ziwiri asanamutumize kundende yozunzirako anthu yoipa kwambiri ya Mauthausen ku Austria. A Eckert atatumizidwa kundendeyi, sanabwererenso kunyumba kwawo. Ngakhale kuti ndi anthu ochepa okha omwe ankamudziwa M’bale Eckert asanamwalire, panopa amadziwidwa ndi anthu ambiri monga munthu yemwe anali ndi chikhulupiriro champhamvu.

Chithunzi chaposachedwapa cha ndende yozunzirako anthu ku Dachau kumene a Max Eckert anatsekeredwa asanawatumize ku Mauthausen.

Ndende yozunzirako anthu ku Mauthausen kumene a Max Eckert anafera.

Malipoti ofotokoza zomwe zinachitika pamoyo wa M’bale Eckert akusonyeza kuti nthawi zonse iye anali wokhulupirika kwa Mulungu. Mu 1935, iye limodzi ndi mkazi wake analipitsidwa chindapusa chifukwa chouza ena zimene ankakhulupirira. Kenako anachotsedwa ntchito chifukwa chokana kunyamula mbendera yomwe inali ndi chizindikiro cha chipani cha Nazi. Mu 1937, bambo Eckert anali mmodzi mwa a Mboni za Yehova olimba mtima pafupifupi 600 omwe anatsekeredwa m’ndende pa zifukwa za ndale ku Dachau. Patatha zaka ziwiri, iwo anasamutsidwa n’kupititsidwa kundende ya ku Mauthausen komwe akaidi osachepera 90,000 anafa chifukwa chochitidwa nkhanza komanso kukhala movutika kwambiri. Pa 21 February, 1940, mkazi wa M’bale Eckert analandira uthenga womwe unanenedwa mopanda ulemu woti: “Mwamuna wako wafa ku ndende. Uyankhule ndi apolisi ngati ukufuna kudziwa zambiri.” Bambo Eckert anafa ali ndi zaka 43.

Poyankhula pamwambowu, Dr. Gabriele Hammermann, omwe ndi mkulu wa malo osungirako mbiri yokhudza nkhanza zomwe zinkachitika pandende yozunzirako anthu ku Dachau, anati: “Ophunzira Baibulo [lomwe ndi dzina limene a Mboni za Yehova ankadziwika nalo pa nthawiyo] anazunzidwa chifukwa chakuti zimene amakhulupirira zinawachititsa kuti asakhale mamembala a bungwe lililonse la chipani cha Nazi, asamachitire Hitler sawatcha, kapenanso kulowa ntchito yausilikali.” Mayiwa ananenanso kuti: “Akaidi ena omwe anali kundendeyi ankalemekeza kwambiri Ophunzira Baibulo chifukwa chakuti ankachita bwino zinthu komanso akaidiwo anatsindika kuti Ophunzira Baibulowo anali okhulupirika ndiponso ankathandiza anthu ena.”

M’bale Wolfram Slupina yemwe amalankhula m’malo mwa a Mboni za Yehova ku Germany, anavomereza kuti anthu omwe anapezeka pa mwambowu sankamudziwa M’bale Eckert. Iwo anati: “Tilibenso ngakhale chithunzi cha a Max Eckert.” Koma iwo ananenanso kuti: Chikwangwani chofotokoza za m’baleyu chikutsimikizira kuti “n’zoonadi kuti [M’bale Eckert] anasonyeza kuti anali wokhulupirika komanso analimba mtima moti sanasiye zomwe amakhulupirira mpaka imfa.”

Sitikukayikira kuti Yehova akukumbukira kukhulupirika kwa a Max Eckert komanso a Mboni za Yehova ena onse omwe anafa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.—Aheberi 6:10.