Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Khoti Lalikulu Kwambiri la Uzbekistan ku Tashkent.

NOVEMBER 8, 2018
UZBEKISTAN

Makhoti Akuluakulu ku Uzbekistan Anagwirizana ndi Zoti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wokhala ndi Mabuku Ofotokoza za Baibulo

Makhoti Akuluakulu ku Uzbekistan Anagwirizana ndi Zoti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wokhala ndi Mabuku Ofotokoza za Baibulo

Kuyambira mu March 2018, makhoti awiri anakhala akuunika milandu yokhudza ufulu wolambira wa a Mboni za Yehova ndipo zimenezi zinachitika kwa miyezi 6. Makhotiwa ndi Khoti Lalikulu Kwambiri ku Uzbekistan komanso khoti loonetsetsa kuti zochita za akuluakulu a boma zikugwirizana ndi malamulo ku Karakalpakstan, lomwe ndi dera loima palokha ku Uzbekistan. Kenako makhotiwa anagamula milanduyo mokomera a Mboniwo. Khoti Lalikulu Kwambiri linasintha zigamulo 4 za makhoti aang’ono zomwe sizinali zokomera abale athu, ndipo khoti loonetsetsa kuti zochita za akuluakulu a boma zikugwirizana ndi malamulo linasintha chigamulo chimodzi.

A Timur Satdanov, m’modzi mwa abale athu omwe Khoti Lalikulu Kwambiri linawapeza kuti si olakwa ku Uzbekistan.

Milandu yambiri imene abale athu anazengedwa inayamba apolisi atakachita chipikisheni ndipo analanda mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo, komanso zipangizo zamakono zomwe zinali ndi Mabaibulo. Chifukwa cha zimenezi, makhoti aang’ono anapeza kuti abale athu ndi olakwa ndipo anawauza kuti alipire chindapusa pogwiritsa ntchito lamulo limene anthu ena amati limaletsa anthu kugawira ena zinthu zachipembedzo. Komabe n’zosangalatsa kuti zigamulo zaposachedwapa zomwe makhoti akuluakulu anapanga, zathandiza kuti abale athu asakhale ndi milandu ndipo sakuyenera kupereka chindapusa.

A Timur Satdanov omwe ndi mmodzi mwa a Mboni omwe poyamba makhoti aang’ono anawapeza kuti ndi olakwa, analembera kalata pulezidenti wa dzikolo yomuyamikira chifukwa cha chigamulo chabwino chimene Khoti Lalikulu Kwambiri linapanga. M’bale Satdanov ananena kuti akuyamikira ndipo anafotokoza kuti iwo limodzi ndi a Mboni ena apitiriza kupempherera “anthu onse apamwamba” kuti akhale ‘ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti akhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso akhale oganiza bwino.’ (1 Timoteyo 2:2) Wachiwiri kwa tcheyamani wa oweruza milandu ku Khoti Lalikulu Kwambiri ananena kuti khotili linalandira kalatayo ndipo linakambirana zomwe zinali m’kalatayo.

A Mboni za Yehova padziko lonse akusangalala ndi zimene zachitikazi ndipo akuthokoza akuluakulu a bomawa. Iwo akuthokoza kwambiri Yehova powatsogolera ndi kuwathandiza “kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino.”—Afilipi 1:7.