Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Ena mwa abale 65 omwe anawatulutsa m’ndende asanamalize kugwira ukaidi, Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea litapereka chigamulo chakuti kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira si mlandu.

MARCH 7, 2019
SOUTH KOREA

A Mboni Onse Omwe Anamangidwa Chifukwa Chokana Usilikali Tsopano Amasulidwa ku South Korea

A Mboni Onse Omwe Anamangidwa Chifukwa Chokana Usilikali Tsopano Amasulidwa ku South Korea

Pa 28 February, 2019, wa Mboni womaliza pa a Mboni amene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali ku South Korea anamutulutsa m’ndende. Abale onse amene anatulutsidwa m’ndende anena kuti ndi osangalala kwambiri chifukwa choti pano ndi omasuka komanso kuti anayesetsa kukhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu.

Pa 1 November, 2018, Khoti Lalikulu Kwambiri ku South Korea linapereka chigamulo chosaiwalika chakuti kukana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira si mlandu, ndipo kuyambira nthawi imeneyo abale 65 atulutsidwa m’ndende. Chigamulochi chinachititsa kuti boma la South Korea lisiye kumanga anthu okana kulowa usilikali, komwe kwakhala kukuchitika kwa zaka 65.

Zimene abale athu a ku Korea anachita posonyeza chikhulupiriro komanso kukhala ndi mtima wosagawanika zikutithandiza kuti nafenso tizionetsa “kulimba mtima kowonjezereka” tikamatumikira mokhulupirika Mfumu yathu ndi Ufumu wake. (Afilipi 1:14) Tikupitirizabe kupempherera abale athu omwe adakali m’ndende ku Eritrea, Russia, Singapore, ndi Turkmenistan.—Aheberi 10:34.