Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Aleksandr ndi Anna Solovyev

JULY 5, 2019
RUSSIA

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Aleksandr Solovyev ndi Wolakwa

Khoti la ku Russia Lagamula Kuti M’bale Aleksandr Solovyev ndi Wolakwa

Lachinayi pa 4 July, 2019, khoti la m’boma la Ordzhonikidzevskiy lomwe lili mumzinda wa Perm’ ku Russia, linalengeza kuti M’bale Aleksandr Solovyev ndi wolakwa ndipo linalamula kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana madola 4,731 a ku America.

M’bale Solovyev anamangidwa pa 22 May, 2018 madzulo pamalo ena okwerera sitima pamene ankafika kuchokera kunja komwe anapita limodzi ndi mkazi wake Anna. Ndiyeno apolisi anamanga M’bale Solovyev ndi unyolo kenako anamutengera kundende ina yongoyembekezera. Apolisi anatenganso Mlongo Solovyev pa galimoto ina yosiyana ndi imene mwamuna wake anakwera. Apolisi anakachita chipikisheni m’nyumba yawo usiku wonse ndipo anatenga zithunzi, zipangizo zamakono, ndiponso Mabaibulo angapo.

Apolisi anafunsa mafunso Mlongo Solovyev ndipo anamuuza kuti azipita atapeza kuti alibe mlandu. Komabe, M’bale Solovyev anamutsegulira mlandu ndipo pa 24 May, anamulamula kuti akhale pa ukaidi wosachoka panyumba mpaka pa 19 November, 2018. Pa nthawi yoyembekezera mlandu wake, m’baleyu anauzidwa kuti alibe ufulu wochita zinthu zina.

Maloya a M’bale Solovyev akapanga apilo chigamulo choti m’baleyu ndi wolakwa. Iwo apemphanso kale Gulu la United Nations Loona za Anthu Omangidwa Popanda Zifukwa Zomveka kuti liunikenso mlanduwu.

Pamene chizunzo chikupitirirabe m’dziko la Russia komanso m’mayiko ena, ‘sitikuchita mantha m’njira iliyonse’ ndi otitsutsa. Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kupatsa tonsefe zinthu zomwe tikufunikira kuti tipirire mpaka tsiku lake lalikulu lachipulumutso litafika.—Afilipi 1:28.