Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Chithunzi chaposachedwapa cha malo osonyeza zomwe zinkachitika kundende yakale yozunzirako anthu ku Ravensbrück omwe ali mumzinda wa Fürstenberg ku Germany.

JANUARY 10, 2019
GERMANY

Chionetsero Chokumbukira Nkhanza Zomwe a Mboni za Yehova Anakumana Nazo ku Germany

Chionetsero Chokumbukira Nkhanza Zomwe a Mboni za Yehova Anakumana Nazo ku Germany

Akuluakulu oyang’anira malo osonyeza zomwe zinkachitika kundende yakale yozunzirako anthu ku Ravensbrück anakonza chionetsero chomwe chizisonyezedwa m’mizinda yosiyanasiyana. Mutu wa chionetserochi ndi wakuti: “Kuzunzidwa Komanso Kuletsedwa kwa Ntchito ya Mboni za Yehova Kundende Yozunzirako Anthu ku Ravensbrück Komanso ku Ndende za ku East Germany.” Chionetserochi chikusonyeza mavuto omwe a Mboni za Yehova ankakumana nawo pa nthawi ya ulamuliro wa maboma atatu a ku Germany. Maboma ake ndi la Weimar Republic lomwe linalamulira kuyambira mu 1918 mpaka 1933, la chipani cha Nazi kuyambira mu 1933 mpaka 1945 ndiponso la German Democratic Republic kuyambira mu 1949 mpaka 1990. (Onani bokosi lakuti: “ Nkhanza Komanso Mavuto Okhudza Zamalamulo pa Nthawi ya Ulamuliro wa Maboma Atatu a ku Germany.”) Chionetserochi chinayamba Lamlungu pa 22 April, 2018, pamalo osonyezera zomwe zinkachitika kundende yakale yozunzirako anthu ku Ravensbrück omwe ali mumzinda wa Fürstenberg ku Germany. M’chaka cha 2019, chionetserochi chidzaonetsedwa m’mizinda ya Erfurt, Rostock, komanso ku Potsdam komwe chidzachitikire m’nyumba ya malamulo ya ku Brandenburg.

Chithunzi cha zimene zinachitikira a Adolf Graf, m’modzi mwa a Mboni amene anazunzidwa ndi maulamuliro a maboma awiri, chinasonyezedwa pa chionetserochi.

Pa chionetserochi padzakhala zithunzi zofotokoza zomwe zinachitikira abale ndi alongo 12 omwe anazunzidwa ku Germany pa nthawi yaulamuliro wa Nazi komanso wachikomyunizimu wa German Democratic Republic. Anthu omwe adzapite kuchionetserochi adzakhala ndi mwayi womvetsera nkhani zojambulidwa, kuwerengedwa kwa makalata otsanzika amene analembedwa ndi a Mboni omwe anaweruzidwa kuti aphedwe, nkhani za m’nyuzipepala ndi mabuku akale a m’nthawi ya ulamuliro wa Nazi. Chionetserochi chikupereka umboni wosonyeza kuti abale athuwa anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, mosiyana ndi anthu ena masauzande ambiri omwe anamangidwa pazifukwa za tsankho, kusiyana maganizo pa nkhani zandale, kapenanso chifukwa cha milandu yongowaganizira.

Polankhula pa mwambo wotsegulira chionetserochi, katswiri wina wambiri yakale, Dr.Detlef Garbe anati: “Kuyambira kalekale, a chipani cha Nazi akhala akudana ndi a Mboni chifukwa choti ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndi ogwirizana ndiponso sanalolere kusiya zimene amakhulupirira. . . . Popeza kuti a Mboni za Yehova amadalira kwambiri lonjezo la Mulungu lakuti adzawapulumutsa komanso amagwirizana kwambiri, zinawathandiza kupeza mphamvu kuti akhalebe okhulupirika ngakhale pa nthawi imene anali m’ndende zozunzirako anthu.”

Masiku anonso a Mboni za Yehova akamatsutsidwa ndiponso maboma akamaletsa ntchito yawo ngati zimene zikuchitika ku Russia, iwo amakhulupirira kuti Yehova adzapitiriza kuwathandiza.—Yesaya 54:17.