Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 19, 2019
DENMARK

Chinthu Chosaiwalika M’mbiri ya Mboni za Yehova: Kutulutsidwa kwa Baibulo Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chiayisilandi

Chinthu Chosaiwalika M’mbiri ya Mboni za Yehova: Kutulutsidwa kwa Baibulo Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chiayisilandi

Pa 19 July, 2019, M’bale Stephen Lett wa m’Bungwe Lolamulira analengeza mosangalala za kutulutsidwa kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu la Chiayisilandi. Baibuloli linatulutsidwa pamsonkhano wamayiko womwe unachitikira ku Copenhagen m’dziko la Denmark.

Lachisanu m’mawa pa nthawi ya msonkhanowu, tcheyamani anauza anthu onse omwe amayankhula Chiayisilandi kuti pa nthawi yopuma masana, apite m’chipinda china chaching’ono cha pasitediyamu imene pamachitikira msonkhanowu. Anthuwo atasonkhana m’chipindacho, M’bale Lett anagawa Mabaibulo kwa abale ndi alongo 341 omwe anali m’chipindacho.

Kwa zaka mahandiredi ambiri, anthu a ku Iceland akhala akugwira ntchito yomasulira Baibulo m’chinenero chawo. Mu 1540, Oddur Gottskálksson anafalitsa Baibulo Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu loyamba la Chiayisilandi. Kuyambira mu 2010, abale ndi alongo athu ku Iceland akhala akugwiritsa ntchito Baibulo la Bible of the 21st Century, lomwe linasindikizidwa ndi kampani ya Mabaibulo ya m’dzikolo. Panopa abale ndi alongo omwe amalalikira m’Chiayisilandi akufunitsitsa kugwiritsa ntchito Baibulo lomwe langotulutsidwa kumeneli pamene akulalikira uthenga wabwino kwa anthu oposa 300,000 oyankhula chinenerochi.

M’bale wina yemwe anamasulira nawo Baibuloli anati: “Ntchito yomasulira Baibulo la Malemba Achigiriki Achikhristu m’Chiayisilandi inatenga zaka 4. Chimene chikupangitsa Baibuloli kukhala losiyana ndi Mabaibulo ena ndi choti, Baibuloli linabwezeretsa dzina la Mulungu lakuti Yehova m’malo onse omwe dzinali liyenera kupezeka. Zimenezi n’zogwirizana ndi pemphero la Yesu lomwe lili pa Yohane 17:26 lomwe limati: ‘Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo.’”

Tikuyamikira kwambiri kuti Yehova akupitiriza kutithandiza pa ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino padziko lonse. Ntchito yomasulira Baibulo ndi imene imatithandiza kwambiri kuti tikwanitse kugwira ntchitoyi. Ndi pemphero lathu kuti anthu ambiri akhale ndi chidwi chofuna kuphunzira zokhudza “zinthu zazikulu za Mulungu” pamene akuwerenga Mawu ake m’chinenero chawo chobadwira.—Machitidwe 2:11.