Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Zotsatira za kugumuka kwa nthaka m’dera la Natonin, ku Mountain Province

AUGUST 14, 2019
PHILIPPINES

Mvula Yamphamvu Kwambiri Yawononga ku Philippines

Mvula Yamphamvu Kwambiri Yawononga ku Philippines

Chakumayambiriro kwa mwezi wa August 2019, ku Philippines kunagwa mvula yamphamvu kwambiri ndiponso kunawomba mphepo yamkuntho zomwe zinachititsa kuti madzi asefukire komanso kuti nthaka igumuke. N’zomvetsa chisoni kuti m’bale wina yemwe ankatumikira monga mpainiya wapadera wakanthawi, anaphedwa ndi nthaka yomwe inagumuka m’dera la Natonin ku Mountain Province. Pa ngozi yomweyi, m’bale winanso yemwe akutumikira monga mpainiya wapadera wakanthawi, anavulala pang’ono. Pa ngozi inanso, mnyamata wazaka 10 anavulala ndi zinyalala koma analandira thandizo lamankhwala loyenera.

Palibe nyumba za abale athu zomwe zinaonongeka kwambiri. Komabe, Nyumba ya Ufumu imodzi ku Negros Occidental inaonongeka pang’ono chifukwa cha mphepo yamphamvu yomwe inachititsa kuti mbali ina ya siling’i igwe.

Ofesi ya nthambi ya ku Philippines ndiponso woyang’anira dera, akutonthoza mabanja a abale athu omwe akhudzidwa, pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

Tili ndi chisoni chifukwa cha imfa ya m’bale wathu ndipo tikupempherera amene aferedwa. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zinthu zopweteka “sizidzakumbukiridwanso.”—Yesaya 65:17.