Pitani ku nkhani yake

SEPTEMBER 5, 2019
UNITED STATES

Mphepo Yamphamvu Kwambiri ya Dorian Yawononga ku Bahamas

Mphepo Yamphamvu Kwambiri ya Dorian Yawononga ku Bahamas

Lamlungu m’mawa pa 1 September, 2019, mphepo yamkuntho ya Dorian, yomwe ndi imodzi mwa mphepo zamphamvu kwambiri pa mphepo zomwe zakhala zikuomba panyanja ya Atlantic Ocean, inaomba pachilumba cha Great Abaco kumpoto kwa dziko la Bahamas. Mphepo ya Dorian inali yoopsa kwambiri chifukwa inkayenda pang’onopang’ono, inkaomba mwamphamvu, komanso inachititsa kuti kugwe mvula yamphamvu. Mphepoyi inadutsa ku Leeward Islands, Puerto Rico, ndi Virgin Islands ndipo pamene inkadutsa, pazilumba zina inawononga pang’ono pomwe pazilumba zina sinawononge.

Ofesi ya nthambi ya United States ikulandirabe malipoti a mmene mphepoyi yakhudzira abale athu komanso zinthu za gulu la Yehova. Pachilumba cha Great Abaco pali mipingo iwiri yomwe ili ndi ofalitsa 46. Pofika pano palibe lipoti losonyeza kuti pali wofalitsa yemwe wavulala. Komabe, Nyumba ya Ufumu yomwe inali imodzi yokhayo pachilumbachi inawonongekeratu.

Pachilumba cha Grand Bahama, pali mipingo 4 komanso ofalitsa 364. Malipoti oyambirira akusonyeza kuti abale athu 196 anathawa m’nyumba zawo ndipo nyumba 22 zinawonongeka pomwe nyumba zitatu zinawonongekeratu.

Mphepoyi isanachitike, ofesi ya nthambi inapereka malangizo kwa oyang’anira madera komanso akulu omwe ali m’madera omwe akhudzidwa ndi mphepo yamkunthoyi. Ofesi ya nthambiyi inapereka malangizo oti abale onse asamukire mumzinda wa Nassau lomwe ndi likulu la dzikoli kapena kumalo ena otetezeka.

Tikupempherera abale ndi alongo athu omwe akuvutika chifukwa cha mphepo yamkunthoyi. Tikudziwa kuti Yehova akuona mavuto omwe akukumana nawo ndipo apitiriza kuwapatsa mphamvu kuti athe kupirira pa nthawi yovutayi.—Salimo 46:1, 2.