Pitani ku nkhani yake

OCTOBER 29, 2019
AZERBAIJAN

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lagamula Mokomera a Mboni 5 Omwe Anakana Kulowa Usilikali ku Azerbaijan

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe Lagamula Mokomera a Mboni 5 Omwe Anakana Kulowa Usilikali ku Azerbaijan

Pa 17 October 2019, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe (ECHR) linagamula kuti abale athu ku Azerbaijan omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira, asaimbidwe mlandu uliwonse. Zimene khotili linagamula n’zofanana ndi zimene makhoti enanso anagamula kuti anthu ali ndi ufulu wokana usilikali ngati kugwira ntchito ya usilikali n’kosemphana ndi chikhulupiriro chawo ndipo sayenera kupatsidwa chilango chilichonse. Aka n’koyamba kuti khoti la ECHR lipereke chigamulo chokomera a Mboni za Yehova ku Azerbaijan.

Chigamulochi chikhudzanso milandu ina yosiyanasiyana yomwe yakhala ikuchitika pakati pa 2008 ndi 2015. Milanduyi ndi yokhudza abale 5 omwe mayina awo ndi: Mushfig Mammadov, Samir Huseynov, Farid Mammadov, Fakhraddin Mirzayev, ndi Kamran Mirzayev. Aliyense wa abalewa anazengedwa mlandu n’kugamulidwa kuti akhale m’ndende ku Azerbaijan chifukwa chokana kulowa usilikali. Khoti linapeza kuti abalewa anakana kulowa usilikali pa chifukwa “chomveka chogwirizana ndi chikhulupiriro chawo.” Pa chifukwa chimenechi, zomwe dziko la Azerbaijan linachitira abale athuwa ndi kuphwanya mfundo za m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Europe. Khotili linanenanso kuti boma la Azerbaijan lisamangopereka mwayi wogwira ntchito zina m’malo mwa usilikali kwa abusa a zipembedzo zina ndi amene akuphunzira za ubusa okha. Kuwonjezera pamenepa, khotili linanenanso kuti boma la Azerbaijan liyenera kulipira abalewa ndalama zomwe akanatha kupanga pa nthawi yonse yomwe akhala m’ndende.

Khotili linanenanso kuti pa nthawi yomwe dziko la Azerbaijan linalowa mumgwirizano wa mayiko a ku Europe, linalonjeza kuti likhazikitsa lamulo lomwe lizipatsa anthu mwayi wogwira ntchito zina za m’dera lawo kupatulapo kulowa usilikali. Malamulo oyendetsera dziko la Azerbaijan amati anthu amene akana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ali ndi ufulu wogwira ntchito zina za m’dera lawo. Komabe, dzikoli silinakhazikitsebe lamulo lolola anthu kutsatira zimenezi ndipo likupitiriza kutsekera m’ndende abale athu chifukwa chokana kulowa usilikali.

Tikukhulupirira kuti zimene Khotili lagamula zichititsa kuti boma la Azerbaijan likhazikitse lamulo lolola anthu kugwira ntchito zina m’malo mwa usilikali. Pakali pano tikupemphera kuti abale athu ku Azerbaijan apitirize kutumikira Yehova molimba mtima.—Salimo 27:14.