Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kuchokera kumanzere: Eldor Saburov ndi mchimwene wake Sanjarbek

AUGUST 7, 2020
TURKMENISTAN

Khoti la ku Turkmenstan Lagamula kuti M’bale Eldor Ndi M’bale Sanjarbek Saburov Akhale Kundende Zaka Ziwiri

Khoti la ku Turkmenstan Lagamula kuti M’bale Eldor Ndi M’bale Sanjarbek Saburov Akhale Kundende Zaka Ziwiri

Pa 6 August 2020, Khoti la ku Turkmenstan linagamula kuti M’bale Eldor ndi M’bale Sanjarbek Saburov akhale kundende zaka ziwiri pa mlandu wokana usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Anthuwa ndi apachibale ndipo wina ndi wa zaka 21 wina wa zaka 25. Khotili linakana pempho la abalewa loti achite apilo. Aka ndi kachiwiri kuti abale awiriwa aweruzidwe pa nkhani imeneyi.

Mu 2016, M’bale Sanjarbek Saburov anakana mwaulemu zoti amulembe usilikali. Zitatero anaweruzidwa kuti asamangidwe koma ayang’aniridwe kwa zaka ziwiri kuti asapalamulenso.

Chaka chotsatira, mng’ono wake wa M’bale Sanjarbek, dzina lake Eldor, anakananso usilikali. Iyeyo anaweruzidwa kuti agwire ntchito kwa zaka ziwiri ndipo 20 peresenti ya malipiro ake azipita kuboma.

Malamulo a m’dzikoli amanena kuti munthu akhoza kuzengedwanso mlandu ngati atakana kachiwiri kulowa usilikali. Mu April 2020, olemba asilikali anawalembanso abalewa koma iwo anakana kupita. Izi zinachititsanso kuti azengedwe mlandu n’kumangidwa.

Makolo a abalewa avutika kwambiri chifukwa cha kumangidwa kwa ana awo. Bambo awo amadwala msana moti satha kugwira bwinobwino ntchito. Mwana wawoyu ndi amene amawathandiza chifukwa choti amalima thonje. Ndiye poti ana awo amangidwa makolowa azisowa chithandizo. Apa tsopano makolowo ndi amene afunika kupereka chithandizo kwa ana awo kundendeko.

Ku Turkmenistan sapereka mwayi wa ntchito ina ngati munthu wakana usilikali. Choncho m’bale wachinyamata akakana usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chake akhoza kumangidwa kwa chaka chimodzi kapenanso 4. Kuwonjezera pa abale awiriwa, palinso abale achinyamata okwana 10 amene anamangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo ku Turkmenistan.

Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kudalitsa abale athu ku Turkmenistan chifukwa cha kulimba mtima kwawo. Onse ayenera kukumbukira zimene Yehova analonjeza Mfumu Asa kuti: “Inuyo khalani olimba mtima ndipo musagwe ulesi pakuti mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.”—2 Mbiri 15:7.