30 DECEMBER, 2021
RUSSIA
M’bale Nikolayev Anapeza Mtendere Chifukwa Chokhulupirira Yehova
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
23 December, 2021
Khoti la m’boma la Abinskiy m’chigawo cha Krasnodar linapeza kuti m’bale Aleksandr Nikolayev ndi wolakwa ndipo anamugamula kuti akakhale m’ndende kwa zaka ziwiri ndi miyezi 6
30 September, 2021
Anakaikidwa m’ndende poyembekezera chigamulo
4 August, 2021
Mlandu wawo unayamba kuzengedwa
26 May, 2021
Anaimbidwa mlandu chifukwa choti anamupeza akukambirana mfundo za m’Baibulo ndi achibale ake komanso anzake. Apolisi anaona kuti umenewu unali “mlandu wophwanya malamulo oyendetsera dzikolo komanso kusokoneza chitetezo”
7 April, 2021
6 koloko m’mawa apolisi a FSB komanso apolisi ena oletsa zachiwawa anabwera kudzafufuza zinthu m’nyumba ya a Nikolayev. Kenako anapita nawo ku polisi komwe anakawapanikiza ndi mafunso ndipo pambuyo pake anawalola kubwerera kunyumba
31 March, 2021
Anawatsegulira mlandu wophwanya malamulo
Zokhudza m’baleyu
Tili ndi chikhulupiriro kuti m’bale Nikolayev komanso abale ndi alongo ena a ku Russia ndi ku Crimea, adzadalitsidwa chifukwa chopitiriza kukhulupirira ndi kudalira Yehova.—Yeremiya 17:7.