31 AUGUST, 2022
RUSSIA
“Yehova Wandipatsa Anzanga Opanda Mantha”
Posachedwa Khoti la Novokuznetsk m’Boma la Kuznetsk, m’Chigawo cha Kemerovo lipereka chigamulo chake pa mlandu wa M’bale Sergey Sushilnikov. Loya waboma sananene chilango chomwe akufuna kuti khotili lipereke kwa m’baleyu.
Nthawi Komanso Zimene Zinachitika
November 2019
Apolisi anayamba kumvetsera zimene M’bale Sushilnikov ankalankhula ndi anthu pa foni yake komanso kuona mavidiyo omwe kamela yapanyumba pa m’baleyu inajambula
3 June, 2021
Mlandu unatsegulidwa
8 June, 2021
Apolisi anakafufuza zinthu m’nyumba ndipo a Sushilnikov ndi akazi awo anawatenga ndi kukawafunsa mafunso
15 July, 2021
Anawalemba pamndandanda wa anthu ochita zinthu zoopsa ndipo ma akaunti awo a kubanki anatsekedwa
8 February, 2022
Anawaimba mlandu wotsogolera gulu lochita zinthu zoopsa ndipo anawauza kuti asapange ulendo ulionse wotuluka m’dzikolo
30 March, 2022
Mlandu unayamba kuzengedwa
Zokhudza M’baleyu
Timalimbikitsidwa kudziwa kuti nthawi zonse Yehova adzapereka thandizo kwa atumiki ake okhulupirika “pa nthawi ya masautso.”—Salimo 46:1.