Pitani ku nkhani yake

Kuchokera kumanzere kupita kumanja: M’bale Yuriy Kolotinskiy, Mikhail Reshetnikov ndi Anatoliy Sarychev

27 MARCH 2024
RUSSIA

Sakuopa Kuzunzidwa Ndipo Akusangalala Podziwa Kuti Yehova Awathandiza

Sakuopa Kuzunzidwa Ndipo Akusangalala Podziwa Kuti Yehova Awathandiza

Posachedwapa, Khoti la m’boma la Leninskiy ku Barnaul m’chigawo cha Altai lilengeza chigamulo chake pamlandu wokhudza abale awa: Yuriy Kolotinskiy, Mikhail Reshetnikov, ndi Anatoliy Sarychev. Loya woimira boma pamlanduwu akuyembekezereka kunena chilango chimene akufuna kuti abalewa apatsidwe.

Zokhudza Abalewa

Tikuthokoza kwambiri chifukwa chokhala ndi abale omwe akusonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro komanso amadalira kwambiri Yehova m’masiku athu ano. Sitikukayikira kuti Yehova apitiriza kuwathandiza chifukwa amakonda komanso sangawaiwale.​—Salimo 25:10.

Nthawi ndi Zochitika

  1. 25 May 2021

    Khoti linatsegulira mlandu Mikhail

  2. 27 May 2021

    Apolisi anakafufuza kunyumba ya Mikhail. Iye ndi Antonina anafunsidwa mafunso. Mikhail analetsedwa kuyenda maulendo ena

  3. 6 October 2022

    Khoti linatsegulira mlandu Anatoliy ndi Yuriy ndipo anaphatikiza milandu yawo ndi wa Mikhail

  4. 7 October 2022

    Anatoliy ndi Yuriy analetsedwa kuyenda maulendo ena

  5. 19 January 2023

    Milandu yawo inayamba kuzengedwa