Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

WEBUSAITI YA JW.ORG

Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW.ORG

Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW.ORG

Mukhoza kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Zina mwa njirazi ndi izi:

  • Pangani dawunilodi pulogalamu ya JW Broadcasting ndipo mungaigwiritse ntchito pa Amazon Fire TV, Apple TV (4th generation), kapena pa Roku.

  • Ngati muli ndi smart TV yokhala ndi pulogalamu yotsegulira zinthu pa intaneti, mukhoza kutsegula webusaiti ya jw.org n’kumaonera mavidiyo. Komabe, pakali pano sizingatheke kuchita zimenezi pa mitundu yonse ya ma smart TV. Choncho simungathe kutsegula mavidiyo pa TV iliyonse.

Mukhozanso kuonera mavidiyo pa TV pogwiritsa ntchito kompyuta kapena chipangizo chanu cham’manja. Zonsezi zimatheka mukafuna kupanga stream pa jw.org kapenanso kuonera mavidiyo omwe mwapanga dawunilodi pachipangizocho.

  • Ngati muli ndi kompyuta ya Apple kapena chipangizo cham’manja komanso chipangizo cha Apple TV, mukhoza kuonera mavidiyo pa TV yanu pogwiritsa ntchito AirPlay. Kuti mudziwe zambiri, pitani pa webusaiti ya Apple pagawo la zokuthandizani.

  • Ngati muli ndi chipangizo cha Google Chromecast, mukhoza kupanga zoti vidiyo izioneka pa TV kudzera pa pulogalamu yotsegulira zinthu pa intaneti ya Chrome. Kuti mudziwe zambiri pitani pawebusaiti ya Google pagawo la zokuthandizani.

  • Mukhoza kulumikiza kompyuta yanu, tabuleti, kapena foni yanu ku TV pogwiritsa ntchito zingwe za HDMI, DVI, VGA, kapena S-Video. Kuti mudziwe njira yabwino yomwe mungasankhe, onani buku la malangizo la kompyuta kapena chipangizo chanu cham’manja ndiponso la TV yanu.