Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 5, 2013
ARMENIA

Dziko la Armenia Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Anthu Amene Akukana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Dziko la Armenia Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Anthu Amene Akukana Kulowa Usilikali Chifukwa cha Zimene Amakhulupirira

Dziko la Armenia likuoneka kuti tsopano lazindikira ufulu wa anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Pa October 23, 2013, akuluakulu a boma anamva pempho la anthu a Mboni okwana 90 loti azipatsidwa ntchito zosagwirizana ndi usilikali ndipo anthu 51 anawapatsa mafomu oti afunsire ntchitozi (akuluakulu a boma aperekanso mafomu kwa anthu a Mboni otsalawa). Kenako akuluakulu a bomawo anapita kundende ya Erebuni ndipo anapereka mafomu a anthu a Mboni 6 amene anamangidwa. Kundendeyi kuli a Mboni okwana 20 ndipo anthu 6 aja anatulutsidwa pa October 24, 2013. Akuluakulu a boma adzatumizanso kundendeko mafomu a anthu a Mboni otsala amene akufuna kupatsidwa ntchito zosagwirizana ndi usilikali ndipo pali chiyembekezo choti anthu amene asankha pulogalamuyi atulutsidwa kundende.

Pulogalamu Yatsopano

Pulogalamuyi inayamba pambuyo poti dziko la Armenia lasintha malamulo okhudza kupereka ntchito zina kwa anthu okana usilikali. Dzikoli linasintha lamuloli pa June 8, 2013, pofuna kugwirizana ndi mfundo zimene mayiko a ku Ulaya amayendera ndipo anayamba kugwiritsa ntchito malamulo atsopanowa pa July 25, 2013. Pa msonkhano wa Nduna za Bungwe la Mayiko a ku Ulaya umene unachitika pa October 2, 2013, pulezidenti wa dziko la Armenia ananena zokhudza kusintha kwa malamuloku. Iye anati: “Anthu amene safuna kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo sadzimangidwanso kapena kuimbidwa mlandu.” Pa October 3, 2013, dziko la Armenia linakhazikitsa lamulo lakuti anthu onse amene ali kundende chifukwa chokana kuchita zinthu potsatira chikumbumtima chawo achotseredwe miyezi 6 pa nthawi imene analamulidwa kukhala m’ndende. Potsatira lamuloli, anthu a Mboni okwana 8 amene anatsala ndi miyezi yosakwana 6 kuti nthawi yawo yotuluka kundende ikwane anatulutsidwa pa October 8 ndi 9, 2013.

Pulogalamu yopatsa ntchito zina anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirirayi ipatsa mwayi anthuwa kugwira ntchito zopititsa patsogolo chitukuko cha dziko lawo popanda kuchita zinthu zosemphana ndi zimene amaphunzira m’Baibulo. Chosangalatsa china n’chakuti ntchito zimene anthuwa azipatsidwa sizikhalanso m’manja mwa asilikali a dziko la Armenia. Anthu azigwira ntchitozi kwa miyezi 36 ndipo aziyenera kugwira maola 48 pa mlungu uliwonse komanso azikhala ndi masiku a tchuthi 10 pachaka. Anthu amene azipempha kugwira ntchitozi aziuzidwa kuti azigwira kumalo oyandikana ndi kumene amakhala ndipo ntchitozi zizikhala zosagwirizana ndi usilikali.

Zimene Zakhala Zikuchitika Kuti Zinthu Zisinthe

Dziko la Armenia litakhala membala wa Bungwe la Mayiko a ku Ulaya mu 2001, linavomera lamulo lakuti mayiko onse amene ndi mamembala atsopano a Bungweli akhazikitse lamulo lopereka ntchito zina kwa anthu okana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Mayikowa anayeneranso kutulutsa kundende anthu onse amene anamangidwa chifukwa chokana kuchita zinthu zosagwirizana ndi chikumbumtima chawo. Ngakhale panali lamuloli, dziko la Armenia linapitirizabe kuimba mlandu komanso kutsekera kundende anyamata a Mboni za Yehova.

Kwa zaka 20 zapitazi, anthu a Mboni za Yehova oposa 450 akhala m’ndende kwa nthawi yaitali, ndipo nthawi zambiri amakhala movutika komanso kuchitiridwa zinthu zankhanza.

Lamulo la Dziko la Armenia lopereka ntchito zina kwa anthu okana kulowa usilikali linayamba kutsatiridwa pa July 1, 2004. Apa zinkaoneka ngati anthu okana kuchita zinthu zina chifukwa cha chikumbumtima chawo zinthu ziyamba kuwayendera bwino. Komabe lamuloli litakhazikitsidwa, ntchito zimene anthuwa ankapatsidwa zinkayang’aniridwa ndi asilikali ndipo ankachita zinthu mwankhanza. Bungwe la Mayiko a ku Ulaya linkanena mobwerezabwereza kuti zimene dziko la Armenia linkachitazi zinali zosagwirizana ndi Mfundo zimene mayiko a M’bungweli amayendera. Mwachitsanzo, M’gawo 1532 (2007), Nduna za Bungwe la Mayiko a ku Ulaya zinanena kuti: “N’zomvetsa chisoni kuona kuti anthu ambiri amene amakana kuchita zinthu zina chifukwa cha chikumbumtima chawo amapatsidwa ntchito zomwenso ndi zosagwirizana ndi chikumbumtima chawo. Pa chifukwachi iwo amasankha kukhalabe kundende m’malo mogwira ntchito zimene anthu okana kulowa usilikali amapatsidwa. Ambiri mwa anthuwa amakhala a Mboni za Yehova.”

Komiti ya Bungwe la United Nations Yoona za Ufulu Wachibadwidwe inadandaulanso kuti dziko la Armenia likupitiriza kumanga anthu a Mboni amene amakana kuchita zinthu zina chifukwa cha chikumbumtima chawo. Pa mawu omaliza a m’gawo 105 (2012), Komitiyi inanena kuti:

“Chipani cholamula chikuyenera kukhazikitsa ntchito zimene anthu onse okana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira azigwira, ndipo zikhale zosagwirizana ndi usilikali ngakhale pang’ono. Ntchitozi zisakhale za nkhanza kapena zokondera pa kagwiridwe ngakhalenso pa kutalika kwa nthawi imene munthu angagwire. Boma likuyeneranso kutulutsa kundende anthu onse amene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali kapena chifukwa chokana kugwira ntchito zimene ndi zogwirizana ndi usilikali.”

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Linathandiza Kwambiri

Mnyamata wina wa Mboni dzina lake Vahan Bayatyan ndi anyamata anzake awiri omwenso ndi a Mboni amene ankaimbidwa mlandu wokana kulowa usilikali, sanathandizidwe atakadandaula ku makhoti a m’dziko la Armenia. Zitatere anyamatawo anapanga apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Pa July 7, 2011, Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya inagamula mlanduwu mokomera a Bayatyan. Aka kanali koyamba kuti Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linene kuti Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya limapatsa ufulu anthu okana kuchita zinthu zina chifukwa cha chikumbumtima chawo. Pambuyo pa chigamulochi, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamulanso milandu ina 4 ndipo zigamulo zonsezi zinapereka ufulu kwa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. a

Anthu amene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linateteza ufulu wawo wokana kuchita zinthu zosagwirizana ndi chikumbumtima chawo: Vahan Bayatyan, Hayk Bukharatyan, Ashot Tsaturyan.

Ngakhale kuti Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya inagamula kuti anthu okana kuchita zinthu zina chifukwa cha chikumbumtima chawo ali ndi ufulu, dziko la Armenia silinatsatire zimenezi. Mwachitsanzo, dzikoli linaimba mlandu anyamata a Mboni za Yehova okwana 29 chifukwa chotsatira chikumbumtima chawo ndipo anaweruzidwa kuti ndi olakwa. Pa anyamatawa, 23 anamangidwa. Kuchokera July 2011 mpaka October 2013, anyamata okwana 86 anatha zaka 168, tikaphatikiza za onse pamodzi, ali m’ndende za ku Armenia. Ena mwa anyamatawa anapanganso apilo ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Zinthu Zimene Zikufunika Kukonzedwa

Anthu omangidwa chifukwa chotsatira chikumbumtima chawo amene akwanitsa nthawi imene analamulidwa kukhala kundende komanso amene ati amalize mu October 2013, akufunitsitsa kuti zimene anawalembera zoti anamangidwapo zifufutidwe. Iwo akufunanso kudziwa ngati anthu amene anaimbidwa mlandu komanso kumangidwa pambuyo pa chigamulo chokhudza mlandu wa a Bayatyan adzapatsidwe ndalama za chipukuta misozi.

Ngakhale kuti dziko la Armenia lakhazikitsa ntchito zimene anthu okana kulowa usilikali azigwira, padakali mavuto ena okhudza ntchito zimene akupereka. Komabe zikuoneka kuti dziko la Armenia tsopano likuyesetsa kulemekeza ufulu wa anthu amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira.

Zimene Zakhala Zikuchitika kuti Pulogalamu Yokhazikitsa Ntchito Zosagwirizana ndi Usilikali Ivomerezedwe

Chaka

Zimene Zinachitika

2001

Dziko la Armenia linakhala membala wa Bungwe la Mayiko a ku Ulaya ndipo linayenera kukhazikitsa lamulo lopereka ntchito zosagwirizana ndi usilikali kwa anthu okana kulowa usilikali

2004

Lamulo lopereka ntchito zina kwa anthu okana kulowa usilikali linakhazikitsidwa, komabe ntchitozi zinkayang’aniridwa ndi asilikali ndipo zimenezi zinapangitsa kuti a Mboni za Yehova asamagwire

2006

Zina ndi zina zokhudza lamulo lopereka ntchito zina kwa anthu okana kulowa usilikali zinasinthidwa komabe panali zinthu zina zogwirizana ndi usilikali zomwe zinali zosayenera kwa anthu a Mboni za Yehova

2011

Pa mlandu umene dziko la Armenia linkaimba a Bayatyan v, Komiti Yaikulu ya Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya inagamula kuti dziko la Armenia linalakwa chifukwa linaphwanya ufulu wotsatira chikumbumtima umene munthu amakhala nawo ndipo Komitiyi inateteza ufulu wa anthu amene amakana kuchita zinthu zina chifukwa cha chikumbumtima chawo

2012

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka zigamulo ziwiri zoweruza kuti dziko la Armenia linaphwanya ufulu wa anthu okana kuchita zinthu zina chifukwa cha chikumbumtima chawo: Bukharatyan v. Armenia ndi Tsaturyan v. Armenia

2013

Pa June 8, 2013, malamulo atsopano anakhazikitsidwa ndipo anayamba kugwira ntchito pa July 25, 2013, zomwe zinathandiza kuti anthu okana kulowa usilikali azipatsidwa ntchito zosagwirizana ndi usilikali ngakhale pang’ono

Pa October 8 ndi 9, dziko la Armenia linatulutsa m’ndende anthu 8 amene anamangidwa chifukwa chokana kuchita zinthu zosemphana ndi chikumbumtima chawo

Pa October 23, akuluakulu a boma anapereka mafomu opempha ntchito zosagwirizana ndi usilikali kwa anthu 57 a Mboni za Yehova, kuphatikizapo anthu a Mboni ena 6 mwa a Mboni 20 amene adakali m’ndende ku Armenia

Pa October 24, dziko la Armenia linatulutsa anthu 6 a Mboni amene anali ku ndende ya Erebuni

a Onani Erçep v. Turkey, nambala 43965/04, 22 November 2011; Bukharatyan v. Armenia, nambala 37819/03, 10 January 2012; Tsaturyan v. Armenia, nambala 37821/03, 10 January 2012; Feti Demirtaş v. Turkey, nambala 5260/07, 17 January 2012.