Pitani ku nkhani yake

DECEMBER 30, 2012
TURKEY

Bungwe la UN Lauza Boma la Turkey Kuti Lizilemekeza Zimene Anthu a M’dzikolo Amakhulupirira

Bungwe la UN Lauza Boma la Turkey Kuti Lizilemekeza Zimene Anthu a M’dzikolo Amakhulupirira

Mayiko ambiri amalemekeza ufulu wa Akhristu mamiliyoni ambiri amene amakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Komiti ya bungwe la UN, yoona za ufulu wachibadwidwe, yapereka chigamulo chakuti dziko la Turkey lizilemekeza zimene anthu a m’dzikolo amakhulupirira.

M’chigamulo chimene komitiyi inapereka pa March 29, 2012, komitiyi inanena kuti anthu awiri a ku Turkey ndi osalakwa pa mlandu imene ankaimbidwa. Anthuwa ndi a Cenk Atasoy komanso a Arda Sarkut ndipo onsewa ndi a Mboni za Yehova. Iwowa anakana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

A Atasoy komanso a Sarkut anayesetsa kufotokozera akuluakulu a boma la Turkey mobwerezabwereza zimene amakhulupirira pa nkhani yolowa usilikali ndipo anapempha kuti awapatse ntchito iliyonse yosagwirizana ndi usilikali. Koma zonsezi sizinaphule kanthu ndipo akuluakulu a boma anakakamizabe anthu a Mboniwa kuti alowe usilikali. Akuluakulu a bomawa anafika poopseza kuti atsegulira mlandu eni yunivesite ina yomwe bambo Sarkut ankaphunzitsa. Izi zinachititsa eni yunivesiteyo kuchotsa ntchito bambo Sarkut.

Pogamula mlanduwu, komitiyi inanena kuti ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene munthu amakhulupirira “ndi mbali ya ufulu wopereka maganizo, wotsatira zimene chikumbumtima chikukuuza komanso wopembedza,” umene umafotokozedwa m’gawo 18 la Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. Kuwonjezera pamenepa, Komitiyi inagamulanso kuti ufulu umenewu “umapatsa mwayi munthu aliyense wokana kulowa usilikali ngati ntchitoyi ikusemphana ndi chipembedzo chake kapena chikhulupiriro chake.

Chigamulochi chinaperekedwa patangopita nthawi yochepa kuchokera pamene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka zigamulo ziwiri zofanana ndi chigamulochi. Pa chigamulo chimodzi mwa zigamulo ziwirizo, Khotili linagamula kuti “kusapezeka kwa ntchito imene munthu angagwire ngati atakana kulowa usilikali m’dziko la Turkey ndi kuphwanya ufulu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima” womwe uli mu Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Kukana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima kunayamba kalekale nthawi imene Chikhristu chinayamba. Munthu wina wolemba mabuku dzina lake E. W. Barnes analemba kuti: “Tikawerenga nkhani zonse zakale mosamala timapeza kuti nthawi imene Marcus Aurelius anakhala ndi moyo, yemwe anali mfumu yachiroma kuyambira mu 161 mpaka mu 180 C.E, palibe Mkhristu amene analowa usilikali ndipo palibe msilikali yemwe anapitirizabe usilikali atalowa Chikhristu.”​—⁠The Rise of Christianity.