Pitani ku nkhani yake

JUNE 11, 2014
TURKEY

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula Mlandu Wina Mokomera Anthu 4 a Mboni ku Turkey

Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya Lagamula Mlandu Wina Mokomera Anthu 4 a Mboni ku Turkey

Pa June 3, 2014, oweruza onse a ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya anagwirizana n’kupereka chigamulo chawo pa mlandu wa anthu 4 a Mboni za Yehova ku Turkey, omwe anakana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Oweruzawo ananena kuti akuluakulu a boma la Turkey anaphwanya mfundo za m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya a pomanga anthuwo. Anthu 4 a Mboniwo, omwe mayina awo ndi Çağlar Buldu, Bariş Görmez, Ersin Ölgün ndiponso Nevzat Umdu, anakana kulowa usilikali chifukwa choti amakhulupirira kwambiri mfundo zimene amaphunzira kuchipembedzo chawo. Polengeza chigamulo chawo, oweruza a khotili anati: “Zimene akuluakulu a boma anachita pomanga anthuwa n’zosagwirizana ndi zimene ziyenera kuchitika m’boma la demokalase. N’zosagwirizananso ndi Gawo 9 la mfundo zimene zili m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.”

Pa March 17, 2008, anthu 4 a Mboniwa anakadula chisamani ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya (pamlandu wakuti Boma la Turkey Likulimbana ndi Buldu ndi Anzake). Iwo anachita izi posumira boma la Turkey kuti silikulemekeza ufulu wawo wolambira Mulungu momasuka. Anthuwo anadandaula kuti bomalo likuchita izi powazunza mobwerezabwereza komanso powatsekera m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali. Kwa nthawi zoposa 30, akuluakulu a boma la Turkey akhala akuitana mobwerezabwereza anthu 4 a Mboniwa kuti akalowe usilikali, ndipo zaka zonse zimene anthuwa akhala m’ndende chifukwa chokana kulowa usilikali n’zoposa 6.

Oweruza a khotili anapitiriza kulengeza chigamulo chawo kuti: “Zimene anachita anthu odandaulawa, omwe ndi a Mboni za Yehova, pokana kulowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ndi chizindikiro champhamvu chosonyeza kuti amakhulupiriradi zimene amaphunzira kuchipembedzo chawo. Khoti lino laona kuti zimene boma likuchita pomanga anthuwa mobwerezabwereza, . . . komanso popitiriza kuwaimba milandu yoopsa, . . . Zikusonyeza kuti bomalo likuphwanya ufulu wa anthuwa wolambira Mulungu momasuka. Ndipotu munthu aliyense ali ndi ufulu wolambira Mulungu momasuka, malinga ndi Gawo 9 la mfundo zimene zili m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.”

Çağlar Buldu

Aka n’kachitatu kuti boma la Turkey lipezeke lolakwa ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, pa milandu yokakamiza anthu kulowa usilikali. Mlandu woyamba unaweruzidwa m’chaka cha 2011, ndipo amene anasumira bomali anali a Yunus Erçep. Kenako mu 2012, a Feti Demirtaş anasumiranso bomali pa nkhani yomweyi, yowakakamiza kulowa usilikali. M’chaka cha 2012 chomwecho, nthambi ya bungwe la UN Yoona za Ufulu Wachibadwidwe inaweruza mlandu wina mokomera anthu awiri a Mboni ku Turkey, pamlandu umene anthuwo anasumira boma la dzikolo chifukwa chowakakamiza kulowa usilikali. Anthuwo ndi a Cenk Atasoy ndiponso a Arda Sarkut.

Pa July 7, 2011, zinthu zinasintha kwambiri m’mayiko onse a ku Ulaya pamene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapereka chigamulo chake pa mlandu wa a Bayatyan ndi Dziko la Armenia. Kwa nthawi yoyamba, oweruza a khotili anaona zoti Gawo 9 la mfundo zimene zili m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya limasonyeza kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira. Izi zikutanthauza kuti mayiko onse amene ali m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya akuyenera kutsatira zimene khotili linagamula. Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya lakhala likuweruza mokomera anthu a Mboni za Yehova pa milandu imene akuluakulu a maboma osiyanasiyana amawakakamiza kuti alowe usilikali. Ina mwa milandu imene khotili linagamula mokomera a Mboni ndi monga mlandu wa a Bayatyan ndi Dziko la Armenia, milandu itatu imene dziko la Turkey linkakakamiza anthu ena a Mboni kuti alowe usilikali, komanso milandu ina yambiri yokakamiza anthu kulowa usilikali m’mayiko a ku Ulaya. Tikaganizira zimene khotili lagamula pa milandu imeneyi, n’zoonekeratu kuti boma la Turkey komanso mayiko ena a ku Ulaya akuyenera kuonanso bwino zimene amachita ndi anthu omwe amawakakamiza kulowa usilikali. Mayikowa akuyeneranso kusintha malamulo awo ena ndi ena kuti agwirizane ndi mfundo zimene zili m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya.

Bambo James E. Andrik, omwe ndi loya amene ankaimira anthu 4 a Mboniwa pa mlanduwu, anati: “Ngakhale kuti panopa palibe munthu wa Mboni amene ali m’ndende ku Turkey chifukwa chokana kulowa usilikali potsatira zimene amakhulupirira, boma likupitirizabe kuimba mlandu anyamata a Mboni amene akukana kulowa usilikali. Tikukhulupirira kuti zimene khoti lagamula posachedwapa pa mlandu wakuti Boma la Turkey Likulimbana ndi Buldu ndi Anzake, zithandiza kuti akuluakulu a bomali asiye kuphwanyira ena ufulu wachibadwidwe, wokana kulowa usilikali. Ndipotu munthu aliyense ali ndi ufulu umenewu, womwe ndi wofunika kwambiri.”

a Gawo 3 limaletsa kuchitira ena nkhanza kapena kuwazunza mwanjira iliyonse; Gawo 6 limanena zoti munthu aliyense akakhala ndi mlandu, ali ndi ufulu woweruzidwa mwachilungamo; Gawo 9 limanena zoti munthu aliyense ali ndi ufulu wokhulupirira kapena kulankhula maganizo ake, kutsatira zimene amakhulupirira, komanso kulowa chipembedzo chimene akufuna ndi kuchita zinthu zogwirizana ndi chipembedzocho.