Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 23, 2015
AZERBAIJAN

Dziko la Azerbaijan Likupitirizabe Kuphwanya Ufulu Wachipembedzo

Dziko la Azerbaijan Likupitirizabe Kuphwanya Ufulu Wachipembedzo

Akuluakulu a dziko la Azerbaijan akupitirizabe kumanga a Mboni za Yehova komanso kuwalipiritsa ndalama zambiri chifukwa chochita misonkhano ya chipembedzo chawo ndiponso kuuza ena zimene amakhulupirira.

Akuimbidwa Mlandu Chifukwa Cholalikira

Pa December 5, 2014, a Mboni awiri, mayi Irina Zakharchenko ndi mayi Valida Jabrayilova ankalalikira m’dera lotchedwa Baku. Mayi Zakharchenko omwe ndi olumala ali ndi zaka 55 komanso ndi amasiye. Pomwe mayi Jabrayilova ali ndi zaka 38 ndipo amasamalira amayi awo. A Mboniwa ankagawira anthu kabuku kakuti Phunzitsani Ana Anu. Kabukuka anakakonza kuti kazithandiza makolo kuphunzitsa ana awo nkhani za m’Baibulo. a

Koma apolisi ananena kuti a Mboniwa ndi olakwa chifukwa ankagawa mabuku othandiza pophunzira Baibulo popanda “chilolezo cha boma.” Mlandu umene azimayiwa anauzidwa kuti anapalamula ndi chimodzimodzi mlandu umene gulu lochita zinthu zophwanya malamulo lingaimbidwe. Chilango cha mlandu wotere chimakhala kulipira ndalama pafupifupi madola 6,690 kapena 8,600 a ku America. b Apo ayi, kutsekeredwa kundende kwa zaka ziwiri kapena 5.

Pa nthawi yomwe apolisi ndi a unduna wa za chitetezo wa m’dzikolo ankafufuza mlanduwu, a Mboniwa ankaitanidwa kukhoti mobwerezabwereza kuti akafunsidwe mafunso. Pa February 17, 2015, a Mboniwa anaitanidwanso ndi apolisi kuti akafunsidwe mafunso koma anadabwa kuuzidwa kuti akufunika kukaonekera kukhoti la Sabail mumzinda wa Baku. Kukhotilo kunalibe aliyense kupatulapo anthu okhawo okhudzidwa ndi mlanduwu.

Wapolisi uja atafotokoza mlandu wa azimayiwa anapempha khoti kuti a Mboniwa amangidwe kaye poyembekezera kuimbidwa mlandu poopa kuti angakapitirizenso kugawa mabuku kapena kuthawa. Koma loya wa a Mboniwa anatsutsa zimene wapolisiyo anapempha chifukwa azimayiwa anali osalakwa ndipo sankavuta pa nthawiyi yomwe ankafunsidwa mafunso. Ngakhale kuti a Mboniwa anali asanapalamuleko mlandu uliwonse, woweruzayo anati a Mboniwa ankasokoneza anthu. Choncho iye anagwirizana ndi zimene wapolisi uja anapempha moti anagamula kuti akhale m’ndende kwa miyezi itatu.

Loya uja anachita apilo ndipo pa February 26, 2015, apolisi anatenga a Mboni aja kuchokera kundende ali omangidwa m’maunyolo. Kenako anawakweza m’galimoto ya magalasi akuda kupita nawo kukhoti la apilo la mumzinda wa Baku. Ulendo unonso kukhotiko kunalibe anthu ena omvetsera mlanduwo, ndipo wapolisi wofufuza mlanduwu komanso akuluakulu a unduna wachitetezo analephera kupereka zifukwa zomveka zochititsa kuti a Mboniwo akhalebe m’ndende. Ngakhale zinali choncho, khotilo linakana kusintha chigamulocho moti mayi Zakharchenko ndi mayi Jabrayilova anatsekeredwanso m’ndende.

Pa March 6, 2015, magulu awiri ochokera ku unduna wa chitetezo anatenga chilolezo kukhoti ndipo anapita kukasecha nyumba za mayi Zakharchenko ndi mayi Jabrayilova. Iwo anatenga mabuku achipembedzo chawo, mabuku ena, kompyuta komanso foni. Pa March 10, 2015, apolisi komanso akuluakulu a unduna wa chitetezo limodzi ndi akuluakulu a bungwe la boma loona za zipembedzo anatenga chilolezo cha khoti ndipo anakafufuza mu Nyumba ya Ufumu (malo amene a Mboni za Yehova amapempheramo) ndiponso nyumba ya mmodzi wa akulu a mumpingomo. Kuwonjezera pamenepa, akuluakulu a unduna wa chitetezo anaitanitsa a Mboni ambiri a ku Baku kuti akawafunse mafunso.

Popeza a Mboni za Yehova sakugwirizana ndi kumangidwa kwa mayi Zakharchenko ndi mayi Jabrayilova, iwo alemba kalata ku gulu lina loona za anthu omangidwa popanda zifukwa zomveka la bungwe la United Nations kuti athandizepo. Loya woimira azimayiwa akukonza zokapempha kukhoti kuti pa nthawi imene azimayiwa akuyembekezera kuimbidwa mlandu, akhale pa ukaidi wosachoka panyumba osati kundende.

Akumangidwa Ndiponso Kulipiritsidwa Chifukwa Chochita Misonkhano ya Chipembedzo Chawo

M’dera lina lotchedwa Ganja, apolisi akhala akulipiritsa anthu amene ankachita misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo ena anamangidwa. Anthu ankalamulidwa kupereka ndalama kuyambira madola 1,433 mpaka 1,911 a ku America.

Mu October 2014, makhoti a mumzinda wa Ganja anapeza kuti a Mboni atatu ndi munthu wina ndi olakwa chifukwa chochita misonkhano yachipembedzochi. Zitatero anawalamula kuti alipire ndalama koma anawamanga atalephera kulipira ndalama zonse. Ngakhale kuti analipirako pang’ono, apolisi anawasungabe m’ndende kwa masiku atatu ndipo ena mpaka masiku 20.

Munthu amene anamangidwa pamodzi ndi a Mboniwa anati: “Ndalamazi kwa ine n’zambiri zedi. . . . Ndinaona kuti sindinkafunika kulipira ndalamazi chifukwa sindinalakwe.” Ndipo a Mboni awiri amene anamangidwawo ananenanso kuti chilangochi chinali chopanda chilungamo ndipo ankawachitira zinthu ngati zigawenga.

Wa Mboni wachitatu yemwe anamangidwa anali mzimayi ndipo anati: “Anandimanga ngakhale kuti banja lathu limavutika kupeza ndalama. Sanaganizirenso zoti ndikusamalira amayi anga omwe ndi olumala ndipo sakwanitsa kuchita chilichonse okha. Analibenso nazo ntchito zoti ndinayamba kupereka ndalama zimene anandilamulazo.”

Anthuwa anamaliza nthawi imene analamulidwa kukhala m’ndende, koma atawatulutsa anawalamulabe kuti amalize kupereka ndalama zonse. Akalephera kumaliza ndalamazi pa nthawi yake, khotilo likhoza kulamula kuti amangidwenso.

Kodi Dziko la Azerbaijan Liyamba Kuchita Zinthu Mwachilungamo?

Akuluakulu a dziko la Azerbaijan akhala akuchita zinthu zosiyanasiyana n’cholinga chofuna kusokoneza ntchito ya Mboni za Yehova. Panopa a Mboni alemba makalata 19 opita ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Makalatawa ndi odandaula za mavuto amene akukumana nawo. Iwo akuyembekezera kuti akuluakulu a dzikoli akonza zinthu ndi kuonetsetsa kuti chilungamo chachitika pa nkhani ya kumangidwa kwa mayi Zakharchenko ndi mayi Jabrayilova. Dziko la Azerbaijan likachita zimenezi lisonyeza kuti likulemekeza ufulu wa anthu, malamulo ndiponso nzika zake.

a Pa August 11, 2014, bungwe la boma loona za zipembedzo m’dziko la Azerbaijan, linavomereza kuti kabukuka, komwe ndi kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, kalowe m’dzikoli.

b Potengera mmene zinthu zinalili m’mwezi wa August 2014, malipiro a anthu ogwira ntchito ku Azerbaijan pa mwezi anali pafupifupi madola 420 a ku America.