Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

7 MARCH, 2017
SOUTH KOREA

Dziko la South Korea Likuchitira a Dong-hyuk Shin Zinthu Zopanda Chilungamo

Dziko la South Korea Likuchitira a Dong-hyuk Shin Zinthu Zopanda Chilungamo

Boma la South Korea limamanga ndi kuika m’ndende anthu amene akukana kulowa ntchito ya usilikali. Komanso limapereka chilango kwa amuna amene akana ntchito ya usilikali omwe mayina awo anaikidwa kale pa m’ndandanda wa mayina a asilikali amene angaitanidwe ngati atafunika.

Ali mnyamata, a Dong-hyuk Shin ankadziwa kuti tsiku lina adzaitanidwa kuti akalowe ntchito ya usilikali. Iwo ankagwira ntchito ya usilikali akauzidwa kuchita zimenezi, ndipo anasiya kugwira ntchitoyi mu 2005. Kenako dzina lawo linaikidwa pa m’ndandanda wa mayina a asilikali amene angathe kuwaitana ngati atafunika ndipo zimenezi zikanachititsa kuti aziitanidwa pafupipafupi kuti azikaphunzira za usilikali kwa zaka 8 zotsatira.

Atawalola kusiya ntchito ya usilikali, a Shin anayamba kuphunzira Baibulo. Zimene ankaphunzira zokhudza mtendere zinawakhudza kwambiri ndipo zinachititsa kuti ayambe kukana ntchito ya usilikali. Ataitanidwa mu March 2006 kuti apite ku maphunziro a asilikali amene amaitanidwa akafunika, anauza akuluakulu a asilikali kuti sapita ku maphunzirowo chifukwa kuchita zimenezi n’kosemphana ndi chikumbumtima chawo.

Palibe Ufulu Wokana Ntchito ya Usilikali Chifukwa cha Chikumbumtima

Dziko la South Korea silipatsa munthu ufulu wokana usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Panopa limaitana a Mboni za Yehova oposa 40 amene ananena kuti sangagwire ntchito ya usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira. Dzikoli limaitana anthuwa kuti akapange maphunziro a asilikali amene amaitanidwa ngati atafunika.

Zimene a Shin ananena kuti sakufuna kupita ku maphunziro a asilikali amene amaitanidwa akafunika sizinamveke, m’malo mwake anawatumizira makalata 30 owaitana m’chaka cha 2006 chokha. A Shin anapitiriza kulandira makalata owaitanawa kwa zaka 7. Kuchokera mu March 2006 kufika mu December 2013, a Shin analandira makalata 118 owaitana kuti akapange maphunziro a usilikali. a A Shin ankakana mwaulemu nthawi iliyonse akaitanidwa, ndipo zimenezi zinachititsa kuti azengedwe milandu komanso kuti apezeke olakwa maulendo 49. Anakaonekera ku makhoti maulendo 69 ndipo zigamulo zonse zimene analandira zinakwana 35.

“Sakanachitira Mwina”

Makhoti sanakayikire kuti a Shin amatsatira chikumbumtima chawo moona mtima. M’chigamulo chimene khoti la m’chigawo cha Ulsan linapereka pa 7 October, 2014, linati: “Ndi zomveka kuti pamene a Dong-hyuk Shin anakhala wa Mboni za Yehova, sakanachitira mwina koma kulolera kuzengedwa mlandu wokana ntchito ya usilikali. Zimenezi zili choncho chifukwa anaona kuti n’zosatheka kugwira ntchito ya usilikali, chifukwa kuchita zimenezi n’kosemphana ndi chikumbumtima chawo komanso zimene amakhulupirira. Sakanatha kuthetsa mavuto amene amabwera chifukwa cha ntchito ya usilikali yomwe imatsutsana ndi chikumbumtima chawo komanso zomwe amaphunzira ku chipembedzo chawo.”

Ngakhale kuti khoti la m’chigawochi linasonyeza kuzindikira mavuto a a Shin, makhoti a m’dziko la South Korea amalephera kupanga zigamulo zomwe n’zosemphana ndi lamulo loti mwamuna aliyense ayenera kuphunzira usilikali. A Shin anagamulidwa ndi makhoti kuti alipire chindapusa choposa madola 13,322 a ku America, komanso anagamulidwa maulendo 6 kuti akakhale m’ndende kwa miyezi yosachepera 6. Pa nthawi zonsezi, a Shin ankauzidwa kuti akhale pa ukaidi wosachoka pakhomo m’malo mokakhala kundende. M’chigamulo china, khoti linalamula a Shin kuti akagwire ntchito yosalipidwa m’dera lawo kwa maola 200.

A Shin ananena kuti: “Ndinali ndi nkhawa kwambiri. Zinkangooneka ngati chiyesochi sichidzatha. Chifukwa chakuti ndimapita ku khoti pafupipafupi, anthu a m’banja langa nawo anali ndi nkhawa. Ndikuganiza kuti mayi anga anavutika kwambiri zaka 9 zimenezo ndipo chifukwa choti amada nkhawa kwambiri zinabweretsa mavuto pa thanzi lawo. Zinkandipweteka kwambiri ndikamaona amayi akuvutika ndi nkhawa chifukwa cha mavuto angawo. Ndinakumananso ndi mavuto a zachuma. Chifukwa choitanidwa mobwerezabwereza kuti ndikalowe usilikali, zinachititsa kuti ndi ziimbidwa milandu ku khoti komanso ndizipezeka kuti ndine wolakwa. Zimenezi zinandichititsa kuti ndisinthe ntchito maulendo 7 chifukwa kupita kukhoti kumachititsa kuti ndizijomba kwambiri ku ntchito.”

Kuphwanya Pangano la Dziko Lonse

A Shin anapanga apilo ku makhoti a ku South Korea koma sanathandizidwe. Khoti Lalikulu Kwambiri linakana ma apilo awo maulendo 4. Chifukwa chosowa thandizo lokhudzana ndi malamulo m’makhoti a ku South Korea, a Shin analemba kalata yodandaula ku Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu mu June 2016. Iwo anafotokoza kuti chifukwa chowaitana mobwerezabwereza kuti akalowe ntchito ya usilikali, kuwaimba milandu ku khoti komanso kuwapeza wolakwa, dziko la South Korea laphwanya udindo wake wolemekeza Pangano la Dziko Lonse la Ufulu wa Anthu ndi wa Zandale. M’kalata yodandaulayo a Shin anatchulamonso zinthu zitatu izi:

  • Anthu amene akana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo akumaitanidwa pafupipafupi kuti akagwire ntchitoyi, ndipo akumapatsidwa chilango mobwerezabwereza akakana kugwira ntchitoyi. Mogwirizana ndi malamulo amene mayiko ambiri amatsatira padziko lonse, kuchita zimenezi ndi kuphwanya ufulu wa anthuwo, wozengedwa mlandu mwachilungamo.

  • Kuitana munthu mobwerezabwereza kuti akapange maphunziro a zausilikali komanso kumuimba milandu, zikutsimikizira kuti cholinga cha akuluakulu a boma ndi kuumiriza anthu kulowa usilikali. Moyo wa a Shin unasokonekera chifukwa choimbidwa milandu, komanso amaonedwa ngati munthu wophwanya malamulo. Zimenezi zili choncho chifukwa a Shin amachita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira zomwe zinachititsa kuti apatsidwe chilango.

  • Chifukwa chakuti a Shin amakana kulowa usilikali chifukwa cha zomwe amakhulupirira, iwo anadandaula kuti ufulu wawo wochita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira komanso ufulu wawo wachipembedzo unaphwanyidwa.

Kuyembekezera Thandizo

A Shin ali ndi chiyembekezo kuti madandaulo awo ayankhidwa chifukwa Komiti Yoona za Ufulu wa Anthu yakhala ikugamula mobwerezabwereza kuti dziko la South Korea likuyenera kumalemekeza ufulu wa anthu amene akukana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. b A Shin akuyembekezera thandizo limene lisonyeze kuganizira anthu amene amakana usilikali akaitanidwa kuti akapange maphunziro a ntchito ya usilikali. A Shin ananena kuti: “Sindikudandaula chifukwa chotsatira chikumbumtima changa komanso zimene ndimakhulupirira, koma ndikudandaula chifukwa chakuti ndavutitsidwa. Ndikukhulupirira kuti boma la South Korea liyamba kuganizira ufulu wa amuna amene amakana kugwira ntchito imene apatsidwa yomwe ikutsutsana ndi chikumbumtima chawo.” A Mboni za Yehova padziko lonse kuphatikizapo a ku South Korea, akugwirizana ndi zimene a Shin ananenazi.

a A Dong-hyuk Shin anaitanidwa maulendo okwana 30 m’chaka cha 2006, maulendo 35 m’chaka cha 2007, maulendo 15 m’chaka cha 2008, maulendo 9 m’chaka cha 2009, maulendo 17 m’chaka cha 2010, komanso m’chaka cha 2011 anaitanidwa maulendo 12. Zaka ziwiri zapitazi maphunziro a usilikali a anthu amene amaitanidwa ngati atafunika sanachitike. Chifukwa cha zimenezi, a Shin sanaitanidwe m’chaka cha 2012 komanso mu 2013.

b Komiti ya United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inapereka zigamulo 5 zosonyeza kuti dziko la South Korea linaphwanya Gawo 18 lokhudza, “ufulu wonena maganizo ako, wotsatira zimene umakhulupirira komanso wachipembedzo”: Yeo-bum Yoon ndi Myung-jin Choi v. Republic of Korea, Communication No. 1321-1322/2004, U.N. Doc. CCPR/C/88/D/1321-1322/2004 (November 3, 2006); Eu-min Jung et al. v. Republic of Korea, Communication No. 1593-1603/2007, U.N. Doc. CCPR/C/98/D/1593-1603/2007 (March 23, 2010); Min-kyu Jeong et al. v. Republic of Korea, Communication No. 1642-1741/2007, U.N. Doc. CCPR/C/101/D/1642-1741/2007 (March 24, 2011); Jong-nam Kim et al. v. Republic of Korea, Communication No. 1786/2008, U.N. Doc. CCPR/C/106/D/1786/2008 (October 25, 2012); and Young-kwan Kim et al. v. Republic of Korea, Communication No.  2179/2012, U.N. Doc. CCPR/C/112/D/2179/2012 (October 15, 2014).