NSANJA YA OLONDA November 2013 | Mabodza Omwe Amalepheretsa Anthu Kukonda Mulungu

Mabodza achipembedzo amene anayamba kalekale amalepheretsa anthu kukonda Mulungu komanso amapangitsa kuti azimuona ngati sakhudzidwa ndi mavuto a anthu. Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu amakhudzidwa ndi mavuto a anthu ndipo si wankhanza?

NKHANI YAPACHIKUTO

Zimene Zimapangitsa Anthu Ena Kuti Asamakonde Mulungu

Kodi mumaona kuti Mulungu sakhudzidwa ndi mavuto anu? Kodi Mulungu ndi wopanda chikondi? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu ena amaganiza choncho.

NKHANI YAPACHIKUTO

Bodza Loyamba: Mulungu Alibe Dzina

Kodi anthu angalidziwedi dzina la Mulungu n’kumalitchula? N’chifukwa chiyani kudziwa dzinali n’kofunika?

NKHANI YAPACHIKUTO

Bodza Lachiwiri: Mulungu ndi Wosamvetsetseka

Chiphunzitso cha Utatu chimapangitsa kuti anthu asadziwe Mulungu komanso kumukonda. Kodi mungakonde munthu amene n’zosatheka kumudziwa bwino kapena amene simungamumvetsetse?

NKHANI YAPACHIKUTO

Bodza Lachitatu: Mulungu ndi Wankhanza

Ambiri amakhulupirira kuti Mulungu amalanga ochimwa kumoto kwamuyaya. Kodi Mulungu ndi wankhanza? Kodi n’chiyani chimachitikira munthu akamwalira?

NKHANI YAPACHIKUTO

Choonadi Chidzakumasulani

Kodi Yesu anatchula mfundo iti imene ingatithandize kuzindikira ngati ziphunzitso zachipembedzo zili zolondola kapena ayi?

CHINSINSI CHA BANJA LOSANGALALA

Kodi Mungatani Kuti Musamakangane ndi Mwana Wanu?

Mwana wanu akulimbana ndi kuti apeze mfundo zimene aziyendera pa moyo wake ndipo zimenezi zingatheke ngati inuyo mutamamulola kufotokoza maganizo ake. Kodi mungamuthandize bwanji?

YANDIKIRANI MULUNGU

“Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna Ndi Mtima Wonse”

Kodi Yehova amakondwera ndi chikhulupiriro chotani? Kodi amapereka bwanji mphoto kwa atumiki ake okhulupirika?

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

‘Anaonedwa Ngati Wolungama Chifukwa cha Ntchito Zake’

Kodi nkhani ya Rahabi ikusonyeza bwanji kuti tonsefe ndife ofunika kwa Yehova? Kodi tingaphunzire chiyani pa chikhulupiriro chake?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Baibulo limenena pa nkhani imeneyi.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Kuti Chipembedzo Cholondola N’chawo Chokha?

Kodi Yesu anati pali misewu yambiri yopita kumoyo wosatha?