NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA October 2014

Magazini ino ili ndi nkhani zophunzila za December 1 mpaka 28, 2014.

Anadzipeleka Mofunitsitsa ku Taiwan

Mboni za Yehova zoposa 100 zatsamukila ku Taiwan kumene kufunikila ofalitsa Ufumu ambili. Ŵelengani zocitika zao za mu ulaliki ndi kuphunzila zimene zawathandiza kupambana.

Khalani ndi Cikhulupililo Cosagwedela mu Ufumu

Yehova anagwilitsila nchito mapangano 6 kutsimikizila kuti Ufumu wake udzakwanilitsa cifunilo cake. Nanga mapangano amenewo angatithandize bwanji kukhala ndi cikhulupililo colimba?

Mudzakhala “Ufumu wa Ansembe”

Pa mapangano 6, mapangano atatu otsilizila amatithandiza kukhulupilila Ufumu wa Mulungu, ndi kulalikila uthenga wabwino wa Ufumuwo kwa ena.

MBILI YANGA

Cocitika Cosaiŵalika pa Utumiki Wanga wa Ufumu

Mildred Olson watumikila Yehova zaka zoposa 75, kuphatikizapo zaka pafupifupi 29 zimene watumikila monga mmishonale ku El Salvador. N’cifukwa ciani amadzimva monga akali wacinyamata?

Muziyamikila Mwai Wanu Wogwila Nchito ndi Yehova

N’ciani cimene cimacititsa kuti alambili a Yehova aziika pambali zofuna zao?

“Ikani Maganizo Anu pa Zinthu Zakumwamba”

N’cifukwa ciani anthu amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi amaika maganizo ao pa zinthu zakumwamba? Nanga angacite bwanji zimenezi?