NSANJA YA MLONDA Na. 4 2016 | Baibulo—Mmene Yapulumukila

Kwa zaka zambili, Baibulo yapulumuka zinthu zosiyanasiyana zimene zikanaiononga. N’cifukwa ciani nkhani ya kupulumuka kwa Baibulo ni yocititsa cidwi?

NKHANI YA PACIKUTO

Nkhani Yofunika Kwambili

Anthu ambili akhala akuikhulupilila kwa nthawi yaitali kupambana mabuku ena onse. Koma kodi Baibulo ni yolondola?

NKHANI YA PACIKUTO

Baibulo Siinawole

Olemba ndi okopela Baibulo aluso anali kuseŵenzetsa gumbwa ndi zikumba polemba uthenga wa m’Baibulo. Kodi mipukutu yakale ya Baibulo masauzande ambili inatetezeka bwanji mpaka masiku ano?

NKHANI YA PACIKUTO

Baibulo Yapulumuka Citsutso

Atsogoleli a ndale ndi a zipembedzo ayesa kuletsa anthu kukhala na Baibulo, kuipulinta, kapena kuimasulila. Kodi Baibulo Yapulumuka Bwanji? Palibe anapambana.

NKHANI YA PACIKUTO

Baibulo Inapulumuka kwa Anthu Ofuna Kusintha Uthenga Wake

Anthu ena acinyengo anayesa kusintha uthenga a m’Baibulo. Kodi anthu amenewo anadziŵika bwanji? Nanga zolinga zao zinakanga bwanji?

NKHANI YA PACIKUTO

Cifukwa Cake Baibulo Yapulumuka

N’ciani cocititsa cidwi ndi buku limeneli?

Kodi Mudziŵa?

N’cinthu cacilendo citi cimene Yesu anacitila anthu akhate? Ni mfundo ziti zimene atsogoleli acipembedzo Aciyuda anali kutsatila pofuna kuthetsa cikwati?

Kodi Zidzatheka Kukhala m’Dziko Lopanda Nkhanza?

Anthu ena athandizidwa kuti aleke kucita nkhanza. Cimene cinawacititsa kusintha, nafenso cingatithandize.

BAIBO IMASINTHA ANTHU

Zinanitengela Nthawi Yaitali Kuti Nisinthe

Kodi munthu wina anathetsa bwanji cizoloŵezi cake cotamba zamalisece n’kukhala ndi mtendele wa m’maganizo?

Kuyelekezela Zinthu Kopindulitsa Kwambili

Machalichi ambili acikhiristu amakhulupilila zinthu zosiyanasiyana ndiponso amaona zinthu mosiyanasiyana. Kodi mungadziŵe bwanji amene amaphunzitsa zoona?

Kodi Baibulo Imakamba Ciani?

Kodi Mulungu amaseŵenzetsa cipembedzo kuti athandize anthu kukhala naye pa ubwenzi?