NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA September 2016
Magazini ino ili na nkhani zophunzila kuyambila mlungu wa October 24 mpaka November 27, 2016.
“Manja Anu Asakhale Olefuka”
Kodi Yehova amalimbikitsa ndi kuthandiza bwanji atumiki ake? Nanga inu mungacite bwanji zimenezi kwa ena?
Cilimikani pa Kulimbana Kuti Mupeze Madalitso a Yehova
Atumiki a Mulungu amakumana ndi mayeselo ambili pamene acilimika kuti apeze madalitso ake. Koma n’zotheka iwo kupambana
Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi
Kodi “mau a Mulungu” amene lemba la Aheberi 4:12 limakamba kuti ndi “amoyo ndi amphamvu” n’ciani?
Kuteteza Uthenga Wabwino Pamaso pa Akulu-akulu a Boma
Tingaphunzile zambili tikaona mmene Paulo anagwilitsila nchito malamulo a boma kuti adziteteze.
Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?
Mfundo za m’Baibulo zingatithandize.
Ubwino Wotsatila Malangizo a Yehova
Mboni za m’dziko la Poland ndi Fiji zinasankha mwanzelu.
Wacicepele, Limbitsa Cikhulupililo Cako
Kodi nthawi zina umakhumbilako zimene ambili amakhulupilila, monga cisanduliko m’malo mwa cilengedwe? Ngati n’conco, magazini ino idzakuthandiza.
Makolo, Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo
Kodi nthawi zina mumaona kuti simungakwanitse? Pali masitepu anayi amene angakuthandizeni.