Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NSANJA YA MLONDA Na. 2 2017 | Kodi Mudzalandila Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse?

MUGANIZA BWANJI?

Kodi mphatso ya Mulungu yopambana zonse imene anatipatsa ni iti?

Baibo imati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha.”Yohane 3:16.

Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza cifukwa cake Mulungu anatuma Yesu padziko lapansi kuti adzatifele. Ifotokozanso mmene tingaonetsele ciyamikilo cathu pa mphatso imeneyo.

NKHANI YA PACIKUTO

Mphatso Yopambana Zonse

Baibo imakamba za mphatso ya mtengo wapatali imene ingabweletse moyo wosatha kwa onse amene ailandila. Kodi pangakhalenso mphatso ina ya mtengo wapali kuposa iyi?

NKHANI YA PACIKUTO

Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse N’cifukwa Ciani ni Yamtengo Wapatali?

N’ciani cimapangitsa mphatso ina kukhala ya mtengo wapatali kupambana ina? Kuganizila zinthu zimenezo kungaticititse kuyamikila kwambili dipo.

NKHANI YA PACIKUTO

Mudzacitapo Ciani pa Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse?

Kodi cikondi ca Khristu cimatikakamiza kucita ciani?

Kuti Munthu Akhale Mtumiki Wacikhristu, Kodi Afunika Kukhala Wosakwatila?

Zipembedzo zina zimafuna kuti azibusa ndi atsogoleli awo azikhala osakwatila. Koma kodi Malemba amati ciani pankhani imeneyi?

Kumasuka mu Ukapolo—Kale na Masiku Ano

Kale, anthu a Mulungu anamasuka mu ukapolo. N’zomvetsa cisoni kuti anthu ofika m’mamiliyoni akali kuvutika ndi ukapolo.

Kupatsa Kumapindulitsa

Kupatsa kumapindulitsa inu ndi ena. Kumalimbikitsa mgwilizano na ubwenzi. Mungacite ciani kuti muzipeleka mokondwela?

Kodi Baibo Imakamba Ciani?

Baibo imakamba kuti “masiku otsiliza” adzakhala “nthawi yapadela komanso yovuta.” Kodi zimenezi zigwilizana ndi nthawi imene tikukhala?