NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA June 2017

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya July 31-August 27, 2017

Kodi Mukumbukila?

Kodi munaŵelenga mosamala magazini aposacedwa a Nsanja ya Mlonda? Yesani kuyankha mafunso awa ozikidwa pa Baibo.

Yehova Amatitonthoza m’Masautso Athu Onse

Ni mavuto ena ati amene Akhristu angakumane nawo m’banja masiku ano? Nanga mungacite ciani kuti mupeze citonthozo kwa Mulungu ngati mukumana ndi mavuto aconco?

Ikani Mtima Wanu pa Cuma Cauzimu

Ni cuma citi cimene tiyenela kuciona kuti n’cofunika ngako? Nanga tingacite ciani kuti tiziciona conco?

Musamaone Cabe Maonekedwe a Munthu

N’ciani cinacitika pamene wa Mboni za Yehova analalikila moleza mtima kwa munthu wokhala mumseu, amene anali woipa m’maonekedwe ndi wosafuna kukhala pamodzi na anzake?

Kodi Mudzakambilana Kuti Muthetse Mkangano ndi Kulimbikitsa Mtendele?

Anthu amafunitsitsa mtendele. Koma akaona kuti ena sakuwalemekeza, ambili amayamba kucita zinthu zosokoneza mtendele. Kodi inu mungacite ciani kuti mupewe kucita zimenezi?

“Udalitsike Cifukwa ca Kulingalila Bwino Kwako”

Awa ni mau amene Davide wa ku Isiraeli wakale anakamba poyamikila Abigayeli. N’ciani cinacititsa Davide kuyamikila mkaziyu? Nanga citsanzo ca mkazi ameneyu citiphunzitsa ciani?

Muziika Maganizo Anu pa Nkhani Yaikulu

Kodi nkhani yaikulu imene ikhudza anthu onse ni iti? Nanga n’cifukwa ciani mufunika kuidziŵa?

Muzicilikiza Ulamulilo wa Yehova

Kodi kudziŵa kuti Yehova ndiye woyenela kulamulila cilengedwe conse kungakupindulitseni bwanji?

Kodi Mudziŵa?

N’cifukwa ciani Yesu anakamba kuti amalonda amene anali kugulitsa ziweto m’kacisi anali “acifwamba”?