NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA February 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa April 2 mpaka 29, 2018.

Tizikhala Okhulupirika Komanso Omvera Ngati Nowa, Danieli ndi Yobu

Anthu okhulupirikawa anakumana ndi mavuto ngati amene timakumana nawo. Kodi n’chiyani chinawathandiza kukhalabe okhulupirika?

Kodi Mumadziwa Yehova Ngati Mmene Nowa, Danieli ndi Yobu Ankamudziwira?

Kodi anthu amenewa anadziwa bwanji Wamphamvuyonse? Kodi kudziwa Mulungu kunawathandiza bwanji? Nanga tingatsanzire bwanji chikhulupiriro chawo?

Kodi Kukhala Munthu Wauzimu Kumatanthauza Chiyani?

Baibulo limafotokoza kusiyana pakati pa munthu wauzimu ndi munthu wakuthupi

Pitirizani Kukula Mwauzimu

Kungophunzira Baibulo si kokwanira kuti tikhale auzimu. Kodi chimafunikanso n’chiyani?