NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) May 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa July 9 mpaka August 5, 2018.

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndinali Wosauka Koma Panopa Ndine Wolemera

Samuel Herd anali wosauka ali wamng’ono koma anadzakhala wolemera kwambiri mwauzimu kuposa mmene ankaganizira.

Mtendere​—Kodi Mungaupeze Bwanji?

Popeza timakhala m’dziko loipa, tiyenera kuchita khama kuti tikhale ndi mtendere. Mawu a Mulungu angatithandize pa nkhaniyi.

Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabereka Zipatso’ Mopirira

Tikhoza kukhumudwa tikamalalikira m’dera limene anthu ambiri samvetsera. Ngakhale zili choncho, tonse tikhoza kubereka zipatso mu utumiki wathu.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kupitiriza Kubala Zipatso Zambiri’?

Tiyenera kukumbukira zifukwa zotichititsa kuti tizilalikira.

Kodi Mumamudziwa Bwino Mdani Wanu?

Timadziwa bwino ziwembu komanso mphamvu za Satana.

Achinyamata, Musasunthike Polimbana ndi Mdyerekezi

Tonsefe tili pa nkhondo yauzimu. Achinyamata ndi amene amaoneka kuti akhoza kupezereredwa koma amayesetsa kuvala zida zonse zankhondo.

Zokolola N’zochuluka

M’dera lina la ku Ukraine, munthu mmodzi pa anthu 4 alionse ndi wa Mboni za Yehova