Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NSANJA YA MLONDA Na. 2 2018 | Kodi Kutsogolo Kuli Ciani?

KODI KUTSOGOLO KULI CIANI?

Kodi munadzifunsapo kuti umoyo wanu na banja lanu udzakhala bwanji kutsogolo? Baibo imakamba kuti:

“Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

Nsanja ya Mlonda ino, idzakuthandizani kumvetsetsa bwino colinga ca Mulungu cokhudza anthu na dziko lapansi, na zimene muyenela kucita kuti mupindule na colinga cimeneci.

 

Kukambilatu Zakutsogolo

Kwa zaka zambili anthu ayesa kukambilatu zimene zidzacitika m’tsogolo. Koma sizimacitika ndendende.

Maulosi Amene Anakwanilitsidwa

Maulosi a m’Baibo ocititsa cidwi, anakwanilitsidwa ndendende.

Umboni Woonetsa Kuti Maulosi a M’baibo Ni Azoona

Cipilala cakale ku Rome cimacitila umboni woonetsa kuti maulosi a m’Baibo ni azoona.

Malonjezo Amene Adzakwanilitsidwa

Maulosi ambili a m’Baibo anakwanilitsidwa kale, koma pali ena okamba za tsogolo lathu amene adzakwanilitsidwa m’tsogolo.

Mungakhale na Moyo Kwamuyaya Padziko Lapansi

Baibo imafotokoza colinga ca Mlengi cokhudza anthu.

Tsogolo Lanu Limadalila pa Zosankha Zanu!

Anthu ena amakhulupilila kuti umoyo wawo unakonzedwelatu ndipo sangausinthe. Kodi zimenezo n’zoona?

“Anthu Ofatsa Adzalandila Dziko Lapansi”

Baibo imatilonjeza kuti idzafika nthawi pamene kuipa na kupanda cilungamo zidzasila.