NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA May 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa July 9 mpaka August 5, 2018.

Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabereka Zipatso’ Mopirira

Tikhoza kukhumudwa tikamalalikira m’dera limene anthu ambiri samvetsera. Ngakhale zili choncho, tonse tikhoza kubereka zipatso mu utumiki wathu.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kupitiriza Kubala Zipatso Zambiri’?

Tiyenera kukumbukira zifukwa zotichititsa kuti tizilalikira.

Kodi Mumamudziwa Bwino Mdani Wanu?

Timadziwa bwino ziwembu komanso mphamvu za Satana.

Achinyamata, Musasunthike Polimbana ndi Mdyerekezi

Tonsefe tili pa nkhondo yauzimu. Achinyamata ndi amene amaoneka kuti akhoza kupezereredwa koma amayesetsa kuvala zida zonse zankhondo.