NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) January 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa 4 March mpaka pa 7 April, 2019

“Usayang’ane Uku ndi Uku Mwamantha, Pakuti Ine Ndine Mulungu Wako”

Onani zifukwa zitatu zotithandiza kuti tizikhala odekha ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto.

Tizitamanda Yehova Mumpingo

Kodi mumavutika kuyankha pamisonkhano? Nkhaniyi ingakuthandizeni kuzindikira vuto lanu komanso kudziwa zimene mmene mungathetsere vutolo.

Kodi Tingateteze Bwanji Mtima Wathu?

Kodi Satana amachita zotani pofuna kusokoneza mtima wathu, nanga tingauteteze bwanji?

Mwambo wa Chikumbutso Umasonyeza Makhalidwe a Mfumu Yakumwamba

Kodi mwambo wa Chikumbutso umasonyeza bwanji kuti Yesu ndi wachikondi, wodzichepetsa komanso wolimba mtima?

Makhalidwe Amene Amatichititsa Kupezeka Pamisonkhano

Kodi kudzichepetsa, chikondi komanso kulimba mtima zimatithandiza bwanji kuti tizipezeka pamisonkhano?

M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira

Dziwani zambiri zokhudza m’Bale Kenneth Cook, Jr.