NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA January 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya March 4-April 7, 2019

“Usayang’ane Uku ndi Uku Mwamantha, Pakuti Ndine Mulungu Wako”

Onani mfundo zitatu zimene zingatithandize kukhalabe odekha pamene takumana na mavuto.

Tamandani Yehova Pakati pa Mpingo

Kodi mumayopa kupeleka ndemanga pa misonkhano? Ngati n’conco, nkhani ino idzakuthandizani kudziŵa zifukwa zake, komanso zimene mungacite kuti muthetse mantha amenewa.

Kodi Tingauteteze Bwanji Mtima Wathu?

N’ciani cimene Satana amacita pofuna kuipitsa mtima wathu? Nanga tingauteteze bwanji?

Zimene Mwambo Wosalila Zambili Umatiphunzitsa Ponena za Mfumu Yathu

Kodi Cikumbutso cionetsa bwanji kuti Yesu ni wodzicepetsa, wolimba mtima, komanso wacikondi?

Kodi Kupezeka pa Misonkhano Kumaonetsa Kuti Ndife Anthu Otani?

Kodi timaonetsa bwanji cikondi, kudzicepetsa, na kulimba mtima pamene tipezeka pa misonkhano ya mpingo?

Ciwalo Catsopano ca Bungwe Lolamulila

Dziŵani zambili zokhudza M’bale Kenneth Cook, Jr.