NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) March 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa May 6 mpaka June 2, 2019

Chikundiletsa Kubatizidwa N’chiyani?

Anthu ena amene aphunzira za Yehova amaopa kubatizidwa. N’chiyani chingawathandize kuti alimbe mtima n’kubatizidwa?

Tizimvetsera Mawu a Yehova

Kodi Yehova amatilankhula bwanji masiku ano? Kodi kumvetsera Mawu a Mulungu kungatithandize bwanji?

Tizichita Zinthu Moganizira Ena

Kodi Yehova ndi Yesu amasonyeza bwanji kuti amaganizira ena? Nanga tingawatsanzire bwanji?

Tizisonyeza Anthu Chifundo Tikakhala mu Utumiki

Tchulani njira 4 zimene tingasonyezere kuti timaganizira ena mu utumiki.

Ubwino​—Kodi Tingatani Kuti Tikhale ndi Khalidweli?

Kodi ubwino n’chiyani? N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala ndi khalidweli?

Mawu Akuti “Ame” Ndi Amtengo Wapatali kwa Yehova

Anthu ambiri amanena ‘ame’ pamapeto pa pemphero. Mawu amenewa amatamanda Mulungu. Kodi mawuwa amatanthauza chiyani, nanga amagwiritsidwa ntchito bwanji m’Baibulo?