NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA June 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya August 5–September 1, 2019

“Samalani Kuti Wina Angakugwileni Ngati Nyama”!

Satana ni katswili posoceletsa anthu. Kodi amayesa bwanji kutikopa kuti tisamvele Yehova?

Gubuduzani Maganizo Aliwonse Otsutsana ndi Kudziŵa Mulungu!

Maganizo athu amasonkhezeledwa na cikhalidwe cathu, maphunzilo, na zokumana nazo mu umoyo. Kodi tingathetse bwanji zizoloŵezi zoipa zimene ‘zinazikika molimba’ mu mtima mwathu?

Dalilani Yehova Pamene Muli na Nkhawa

Kukhala na nkhawa yopambanitsa kapena yamtatakuya kungatidwalitse na kutifooketsa. Tingaphunzile zambili mwa kuganizila mmene Yehova anathandizila atumiki ake akale kuthetsa nkhawa

Thandizani Ena Kulimbana na Nkhawa

Loti, Yobu, ndi Naomi anatumikila Yehova mokhulupilika. Ngakhale n’telo, nthawi zina iwo anali kukumana na mavuto komanso kukhala na nkhawa. Kodi tingaphunzilepo ciani pa zimene zinawacitikila

Mmene Tingadzitetezele ku Msampha wa Satana

Msampha wa kutamba zamalisece wakola atumiki ambili a Mulungu. Kodi tingapewe bwanji mcitidwe wodetsa umenewu?

Kuŵelenga Mpukutu Wamakedzana Wakupsa na Moto

Mu 1970, akatswili ofukula zinthu zakale, anapeza mpukutu wakupsa na moto ku Ein Gedi, m’dziko la Israel. Poseŵenzetsa makina amakono ounikila zinthu, akatswili akwanitsa kuŵelenga mpukutuwu. Kodi n’ciani cimene anapeza pambuyo pouŵelenga?