NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA July 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya September 2-29, 2019

Konzekelani Cizunzo Pali Pano

Kodi tingacite ciani kuti tikhale olimba mtima kwambili na kuti tipilile citsutso?

Musaleke Kulambila Yehova pa Nthawi ya Ciletso

Kodi tiyenela kucita ciani ngati boma latiletsa kulambila Yehova?

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzila”

N’cifukwa ciani nchito yopanga ophunzila ni yofunika kwambili? Nanga ni malangizo ati amene angatithandize pogwila nchito imeneyi?

Kulalikila Anthu Osapembedza Mowafika pa Mtima

Kodi tingawathandize bwanji anthu osapembedza kuyamba kukonda Mulungu mpaka kukhala ophunzila a Khristu?

MBILI YANGA

Yehova Wanidalitsa Kwambili Kuposa Mmene N’nali Kuyembekezela

Kutumikila mu Africa monga mmishonale kwathandiza M’bale Manfred Tonak kukhala na makhalidwe ambili abwino monga kuleza mtima komanso kukhala wokhutila.

Kodi N’zoona Kuti Yesu Ananifela Ine?

Kodi nthawi zina mumadziona kukhala wosafunika? N’ciani cingakuthandizeni mukakhala na maganizo otelo?