GALAMUKANI! Na. 1 2020 | Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa

Masiku ano anthu ambiri amavutika ndi nkhawa. Komabe pali zimene mungachite kuti musamakhale ndi nkhawa kwambiri.

Kodi Mumavutika Kwambiri ndi Nkhawa?

Pali zimene mungachite kuti musamavutike kwambiri ndi nkhawa.

Zomwe Zimachititsa Kuti Anthu Azikhala ndi Nkhawa

Werengani magaziniyi kuti mudziwe zinthu zina zomwe zimachititsa munthu kukhala ndi nkhawa ndipo muone ngati pali zomwe inunso zimakuchitikirani.

Zimene Zimachitika Munthu Akakhala ndi Nkhawa

Aliyense amakhala ndi nkhawa. Werengani nkhaniyi kuti muone mmene nkhawa ingakhudzire thanzi lanu.

Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?

Onani njira zomwe mungatsatire kuti musamakhale ndi nkhawa kapena kuti mukwanitse kuzichepetsa.

N’zotheka Kudzakhala ndi Moyo Wopanda Nkhawa

Anthufe sitingakwanitse kuthetseratu nkhawa. Koma Yehova angakwanitse kuchita zimenezi.

“Mtima Wodekha Ndiwo Moyo wa Munthu”

Mawu amenewa omwe amapezeka pa Miyambo 14:​30, amasonyeza kuti mfundo za m’Baibulo ndi zothandiza nthawi zonse.