NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA March 2020

Magazini ino ili na nkhani zophunzila kuyambila pa May 4-31, 2020.

Kukonda Yehova na Kum’yamikila Kudzakusonkhezelani Kubatizika

Kukonda Yehova kungakusonkhezeleni kubatizika. Koma kodi n’ciani cingakulepheletseni kubatizika?

Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?

Mayankho anu pa mafunso amene ali m’nkhani ino adzakuthandizani kuona ngati ndimwe wokonzeka kubatizika.

MBILI YANGA

“Ife Tilipo! Titumizeni”

M’bale Jack na mlongo Marie-Line afotokoza zimene zinawasonkhezela kuyamba utumiki wa nthawi zonse, komanso zimene zinawathandiza kujaila umoyo watsopano akapatsidwa utumiki watsopano.

Kodi Nthawi Yoyenela Kukamba ni Iti?

Onani zitsanzo za m’Baibo zimene zingatithandize kudziŵa nthawi yoyenela kukamba na nthawi yoyenela kukhala cete.

Muzikondana Kwambili

Yesu anakamba kuti cikondi n’cimene cimadziŵikitsa Akhristu oona. Kodi cikondi cimatithandiza bwanji kukhala anthu obweletsa mtendele, opanda tsankho, komanso oceleza?

Kodi Mudziŵa?

Kuwonjezela pa zimene Baibo imakamba, kodi palinso umboni wotani woonetsa kuti Aisiraeli anakhalako akapolo ku Iguputo?

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

Kodi apolisi aciyuda a pa kacisi anali ndani? Nanga anali kugwila nchito yanji?