NSANJA YA OLONDA—YOPHUNZIRA March 2020

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa May 4-31, 2020.

Munthu Amabatizidwa Chifukwa Chokonda Yehova Komanso Kumuyamikira

Munthu amafuna kubatizidwa akayamba kukonda kwambiri Yehova. Koma kodi n’chiyani chingamulepheretse kuchita zimenezi?

Kodi Ndinu Okonzeka Kubatizidwa?

Zimene mungayankhe pa mafunso amunkhaniyi zingakuthandizeni kudziwa ngati mwakonzeka kubatizidwa kapena ayi.

Kodi Mumadziwa Nthawi Yoyenera Kulankhula?

Onani zitsanzo za m’Baibulo zotithandiza kudziwa nthawi yoyenera kulankhula ndi yoyenera kukhala chete.

Muzikondana Kwambiri

Yesu ananena kuti chikondi ndi chizindikiro cha Akhristu oona. Kodi chikondi chimatithandiza bwanji kukhala mwamtendere ndi ena, opanda tsankho komanso ochereza?