Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NSANJA YA MLONDA Na. 1 2021 | N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela?

Kodi nthawi zina mumaona monga Mulungu sanayankhe mapemphelo anu? Ngati n’conco, dziŵani kuti si imwe mwekha. Ambili apemphelapo kwa Mulungu kuti awathandize pa vuto lawo, koma vutolo silinathe. Nkhani za m’magazini ino zifotokoza cifukwa cake tiyenela kukhulupilila kuti Mulungu amamvetsela mapemphelo athu, cifukwa cake sayankha mapemphelo ena, komanso mmene mungapemphelele kuti azimvetsela mapemphelo anu.

 

Zimene Anthu Amakamba Pankhani ya Kupemphela

Kodi pemphelo ni mphatso yapadela yocokela kwa Mulungu, kapena ni mwambo cabe wopanda phindu?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Athu?

Baibo imatitsimikizila kuti Mulungu amamvetsela mapemphelo athu ngati timupempha m’njila yoyenela.

N’cifukwa Ciani Mulungu Sayankha Mapemphelo Onse?

Baibo imatiuza mapemphelo amene Mulungu amayankha komanso amene sayankha.

Mungapemphele Bwanji Kuti Mulungu Azimva Mapemphelo Anu?

Kambani na Mulungu kulikonse komanso pa nthawi iliyonse, mokweza kapena camumtima. Yesu anatiphunzitsa zimene tingakambe popemphela.

Kodi Mapemphelo Angakuthandizeni Bwanji?

Kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji kupilila mavuto?

Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Anu?

Baibo imakamba kuti mukapemphela kwa Mulungu, iye amamva ndipo amafuna kukuthandizani.