Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?

A Mboni za Yehova akupezeka padziko lonse ndipo ndi a mafuko komanso zikhalidwe zosiyanasiyana. Kodi n’chiyani chimathandiza kuti anthu onsewa azichita zinthu mogwirizana?

Kodi Chifuniro cha Mulungu N’chotani?

Mulungu akufuna kuti chifuniro chake chichitike padziko lonse lapansi. Kodi chifuniro chakecho n’chotani, nanga masiku ano ndi ndani amene akuphunzitsa ena zokhudza chifunirocho?

PHUNZIRO 1

Kodi a Mboni za Yehova ndi Anthu Otani?

Kodi ndi anthu angati a Mboni za Yehova amene inuyo mumawadziwa? Kodi mumadziwa zotani zokhudza anthuwo?

PHUNZIRO 2

N’chifukwa Chiyani Timatchedwa Mboni za Yehova?

Dziwani zifukwa zitatu zimene zinatichititsa kutenga dzina lakuti Mboni za Yehova.

PHUNZIRO 3

Kodi Chinachitika N’chiyani Kuti Choonadi cha M’Baibulo Chidziwikenso?

N’chifukwa chiyani tikukhulupirira kuti tikumvetsa molondola zimene Baibulo limaphunzitsa?

PHUNZIRO 4

N’chifukwa Chiyani Tinatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano?

N’chiyani chimachititsa Mabaibulo ena kukhala apadera kwambiri?

PHUNZIRO 5

Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Mudzasangalale Nazo Pamisonkhano Yathu Yachikhristu?

Timasonkhana pamodzi kuti tiphunzire Malemba komanso kuti tilimbikitsane. Fikani pamisonkhano yathu ndipo tidzakulandirani ndi manja awiri!

PHUNZIRO 6

Kodi Timapindula Bwanji Tikamasonkhana ndi Akhristu Anzathu?

Mawu a Mulungu amalimbikitsa Akhristu kuti azisonkhana pamodzi. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene kusonkhana pamodzi kumatithandizira.

PHUNZIRO 7

Kodi Misonkhano Yathu Imachitika Bwanji?

Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti misonkhano yathu imachitika bwanji? Sitikukayikira kuti mungasangalale kwambiri ndi mmene timaphunzirira Baibulo ngati mungafike pamisonkhano yathu.

PHUNZIRO 8

N’chifukwa Chiyani Timavala Bwino Tikamapita Kumisonkhano Yathu?

Kodi zimene timasankha kuvala zimakhudzana ndi kulambira kwathu Mulungu? Onani mfundo za m’Baibulo zimene timatsatira pa nkhani ya kavalidwe ndiponso kudzikongoletsa.

PHUNZIRO 9

Kodi Tingatani Kuti Tizikonzekera Bwino Misonkhano?

Kukonzekera bwino misonkhano kungakuthandizeni kuti muzipindula kwambiri ndi misonkhanoyo.

PHUNZIRO 10

Kodi Kulambira kwa Pabanja N’chiyani?

Nkhaniyi ikuthandizani kudziwa mmene kulambira kwa pabanja kungakuthandizireni kuti mukhale pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Mulungu komanso ndi banja lanu.

PHUNZIRO 11

N’chifukwa Chiyani Timakhala ndi Misonkhano Ikuluikulu?

Chaka chilichonse, timachita misonkhano ikuluikulu. Kodi kupezeka pamisonkhano imeneyi kungakuthandizeni bwanji?

PHUNZIRO 12

Kodi Ntchito Yathu Yolalikira za Ufumu Imachitika Motani?

Timagwira ntchito yolalikira motsanzira mmene Yesu ankachitira pamene anali padziko lapansi. Kodi zina mwa njira zolalikirirazo ndi ziti?

PHUNZIRO 13

Kodi Mpainiya Amachita Chiyani?

Anthu ena a Mboni za Yehova amagwira ntchito yolalikira kwa maola 30, 50, kapena kuposa pamenepa, mwezi uliwonse. N’chifukwa chiyani iwo amasankha kuchita zimenezi?

PHUNZIRO 14

Kodi Apainiya Ali Ndi Mwayi Wochita Maphunziro Otani?

Kodi anthu amene anadzipereka kuti nthawi zonse azigwira ntchito yolalikira kapena ntchito ina yothandizira kulalikira, ali ndi mwayi wochita maphunziro ati?

PHUNZIRO 15

Kodi Akulu Amathandiza Bwanji Mpingo?

Akulu ndi amuna odziwa zambiri omwe atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali ndipo amatsogolera mumpingo. Kodi akuluwa amachita zotani?

PHUNZIRO 16

Kodi Atumiki Othandiza Ali Ndi Udindo Wotani?

Atumiki othandiza amathandiza kwambiri mumpingo kuti zinthu ziziyenda bwino. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene ntchito zawo zimathandizira anthu onse amene afike pamisonkhano.

PHUNZIRO 17

Kodi Oyang’anira Dera Amatithandiza Bwanji?

N’chifukwa chiyani oyang’anira dera amachezera mipingo? Kodi mungatani kuti muzipindula ndi kuchezera kwa oyang’anira dera?

PHUNZIRO 18

Kodi Timathandiza Bwanji Abale Athu Amene Ali M’mavuto?

Pakachitika tsoka, nthawi yomweyo timayamba kuthandiza abale athu omwe akhudzidwa ndi tsoka powapatsa zinthu zofunika pamoyo komanso timawalimbikitsa mwauzimu. Kodi timachita bwanji zimenezi?

PHUNZIRO 19

Kodi Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru ndani?

Yesu analonjeza kuti adzaika kapoloyu kuti azidzapereka chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera. Kodi kapoloyu akupereka bwanji chakudyachi?

PHUNZIRO 20

Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?

M’nthawi ya atumwi panali kagulu kakang’ono ka atumwi ndi akulu omwe anali ngati bungwe lolamulira la mpingo wachikhristu. Nanga bwanji masiku ano?

PHUNZIRO 21

Kodi Beteli N’chiyani?

Beteli ndi malo apadera kwambiri ndipo m’malowa mumachitika ntchito yofunika zedi. Dziwani zinthu zambiri zokhudza anthu omwe amagwira ntchito kumaofesi amenewa.

PHUNZIRO 22

Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?

Alendo amaloledwa kudzaona maofesi athu. Tikukupemphani kuti inunso mupite kukaona zimene zimachitika kumeneko!

PHUNZIRO 23

Kodi Ntchito Yolemba Ndiponso Kumasulira Mabuku Athu Imayenda Bwanji?

Timasindikiza mabuku m’zinenero zoposa 700. N’chifukwa chiyani timamasulira mabuku athu m’zinenero zambiri?

PHUNZIRO 24

Kodi Ndalama Zothandizira pa Ntchito Yathu Yapadziko Lonse Zimachokera Kuti?

N’chiyani chomwe chimasiyanitsa gulu lathu ndi zipembedzo zina pa nkhani ya kagwiritsidwe ntchito ka ndalama?

PHUNZIRO 25

N’chifukwa Chiyani Timamanga Nyumba za Ufumu Ndipo Timazimanga Bwanji?

N’chifukwa chiyani malo athu olambirira amatchedwa Nyumba ya Ufumu? Werengani mmene nyumba zimenezi zimathandizira anthu a m’mipingo ya Mboni za Yehova.

PHUNZIRO 26

Kodi Tingathandize Bwanji Kuti Nyumba Yathu ya Ufumu Izioneka Bwino?

Nyumba ya Ufumu yosamalidwa bwino imapangitsa kuti Mulungu azimalemekezedwa. Kodi mpingo umakonza zotani kuti Nyumba ya Ufumu yawo izikhala yooneka bwino?

PHUNZIRO 27

Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?

Kodi mukufuna kufufuza nkhani kuti mudziwe zambiri zokhudza Baibulo? Kaoneni laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu!

PHUNZIRO 28

Kodi Pamalo Athu a pa Intaneti Pali Zinthu Zotani?

Mungadziwe zinthu zambiri zokhudza ifeyo komanso zimene timakhulupirira ndipo mungapeze mayankho okhudza Baibulo.

Kodi Mukufuna Kuchita Zimene Yehova Amafuna?

Yehova Mulungu amakukondani kwambiri. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumafuna kusangalatsa Mulungu pamoyo wanu wa tsiku ndi tsiku?