Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2014

Werengani zochitika zapadera zochokera kumayiko a Sierra Leone ndi Guinea komanso zinthu zolimbikitsa zimene zachitika padziko lonse.

Lemba la Chaka cha 2014

Lemba lathu la chaka cha 2014 ndi lakuti “Ufumu Wanu Ubwere.”—Mateyu 6:10

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Mulimbikitsidwa kwambiri mukawerenga kalata yachikondiyi yochokera ku Bungwe Lolamulira.

Gulu la Yehova Likupita Patsogolo

Mmene ntchito yosamutsa likulu lathu kuchoka ku New York City ikuyendera, zikusonyezeratu kuti Yehova akutitsogolera.

WEBUSAITI YA JW.ORG—Ikuchitira “Umboni ku Mitundu Yonse”

Webusaiti yathu ikuthandiza kuti anthu a “mitundu yonse” amve uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.”

Akusangalala ndi LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower

Anthu amene akugwiritsa ntchito laibulale imeneyi anatitumizira makalata oyamikira.

Ana Akusangalala ndi Mavidiyo a Makatuni

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene mavidiyowa akuthandizira ana ndiponso mabanja padziko lonse.

Chionetsero Chosangalatsa cha Mbiri ya Mboni za Yehova

Werengani nkhaniyi kuti mumve za chionetsero chatsopano cha mbiri ya Mboni za Yehova komanso zina zimene zachitikira Akhristu.

Lipoti la Milandu

Malipoti a milandu yochokera m’mayiko 12 amenewa akusonyeza kuti mayiko ambiri akupha ufulu wolambira wa Mboni za Yehova.

Malipoti Apadera—Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana

A Mboni za Yehova akuyesetsa kumanga malo abwino olambirira Mulungu.

Mwambo Wopereka Nthambi

Onani zinthu zina zosangalatsa zimene zinachitika pa mwambowu m’mayikowo

Africa

Anthu ambiri ku Africa akuphunzira Baibulo ndipo akusintha kwambiri makhalidwe awo. Werengani za munthu amene anasiya kumwa mowa mwauchidakwa komanso kusuta ndudu 60 patsiku.

North ndi South America

Nkhanizi zikusonyeza kuti ntchito yolalikira imayenda bwino ngati timathandiza ena komanso timalalikira ngakhale kuti timatsutsidwa.

Asia ndi Middle East

Khama limene abale akusonyeza pa ntchito yolalikira likubala zipatso. Werengani nkhaniyi kuti muone zimene munthu wina anachita kuti athandize munthu yemwe ndi wosamva, wosaona komanso wosalankhula, kuti adziwe zoti Mulungu amamukonda.

Europe

Anthu amadana ndi Mboni chifukwa cha zabodza zomwe anauzidwa. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene pulogalamu ya pawailesi inathandizira anthu kuti asiye kudana ndi Mboni za Yehova.

Oceania

Kulemba makalata ndi njira ina yomwe choonadi cha m’Baibulo chikufalitsidwira mumzinda wa Christchurch ku New Zealand. N’chifukwa chiyani ena amatchula makalatawa kuti “Makalata Ochokera kwa Mulungu?”

Mfundo Zachidule Zokhudza Mayiko a Sierra Leone ndi Guinea

Werengani kuti mudziwe mmene mayikowa alili, anthu ake, chipembedzo komanso zilankhulo.

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 1)

Mu Mboni yobatizidwa inafika ku Freetown ndipo anthu ambiri ankafuna kuphunzira Baibulo.

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 2)

Atsogoleri achipembedzo ankafuna kusokoneza anthu a Mulungu koma Yehova ‘anawabwezera zoipa zawo.’

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 3)

Abale ndi alongo a mumpingo wa ku Freetown “anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu.”

“Mufa Chaka Chisanathe”

Kawiri pa mlungu, Zachaeus ankayenda mtunda wa makilomita 8 kudutsa phiri, kuti akasonkhane ndi Mboni za Yehova. Kodi anadziwa bwanji kuti wapeza chipembedzo choona?

Anamupatsa Dzina Loti “Baibulo” Brown

William R. Brown analalikira kuzilumba za Caribbean ndi ku West Africa. Werengani kuti mudziwe chifukwa chake ankaona kuti ali ndi mwayi waukulu kwambiri.

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Kukhala Olungama’—Dan. 12:3. (Gawo 1)

Ntchito yolalikira inawonjezeka kwambiri. Amishonale anathandiza anthu ambiri kuyamba kuphunzira choonadi.

Ankafunitsitsa Kuionera

Mu 1956, filimu ya ‘The New World Society in Action’ inaonetsedwa ku Freetown, Sierra Leone. Kodi anthu anabwera kudzaionera?

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kukhala Olungama’—Dan. 12:3. (Gawo 2)

Anthu ku Sierra Leone amadziwa kuti Mboni za Yehova zimalemekeza ukwati.

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kukhala Olungama—Dan. 12:3. (Gawo 3)

N’chifukwa chiyani anthu andale amene anali m’gulu la Poro ankafuna kuti boma liletse ntchito ya Mboni za Yehova?

Magulu Ochita Zamizimu

Kodi anthu a ku West Africa amakhudzidwa bwanji ndi zochita za maguluwa?

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kukhala Olungama’—Dan. 12:3. (Gawo 4)

Pothandiza anthu kutumikira bwino Mulungu, mipingo imachita makalasi ophunzitsa kuwerenga ndi kulemba. Popeza kuti anthu ambiri anaphunzira kuwerenga, panafunika kumasulira mabuku ambiri.

Baji Yawo Inali Ngati Pasipoti

Kodi zinatheka bwanji kuti abale akachite nawo msonkhano m’dziko la Guinea ngakhale kuti analibe ziphaso kapena mapasipoti?

Yehova Wandithandiza

Jay Campbell, yemwe ndi wolumala, ankafuna kupita ku phunziro la Baibulo la mpingo. Iye ananena kuti adzayenda yekha pogwiritsa ntchito matabwa ake. Kodi anatha kupita?

Kuyambira mu 1991 mpaka 2001 ‘Ng’anjo ya Masautso’—Yes. 48:10 (Gawo 1)

Pa nthawi ya nkhondo, a Mboni komanso anthu ena analandira chithandizo komanso kulimbikitsidwa ndi Malemba. N’chiyani chinawathandiza kukhala olimba mtima?

Kuyambira mu 1991 mpaka 2001 ‘Ng’anjo ya Masautso’—Yes. 48:10 (Gawo 2)

Pa nthawi ya nkhondo, a Mboni za Yehova “anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.”

Kusiya Usilikali N’kuyamba Upainiya Wokhazikika

Mnyamata wina, yemwe anali m’gulu la zigawenga, anakumbukira kuti anthu anamulandira bwino pamene anapita ku msonkhano wa Mboni za Yehova. N’chiyani chinamulimbikitsa kusintha?

Tinapulumuka M’manja mwa Zigawenga

Nkhondo itayamba mu 1991, abale ndi alongo ambiri anapulumuka m’manja mwa zigawenga zomwe zinkapha anthu ku Pendembu. Kodi zinatheka bwanji?

Wa Nsanja ya Olonda

Kodi m’bale wina ankatha bwanji kunyamula zinthu ku Freetown kukapereka kwa abale ku Conakry m’dziko la Guinea pa nthawi ya nkhondo?

Ndinapeza Chinthu Chamtengo Wapatali Kuposa Dayamondi

Tamba Josiah asanakhale wa Mboni ankagwira ntchito mumgodi wa dayamondi. N’chifukwa chiyani amanena kuti anapeza chinthu chamtengo wapatali kuposa dayamondi?

Kuyambira mu 2002 mpaka 2013 (Gawo 1)

Nkhondo yapachiweniweni itatha, mipingo inakhazikitsidwa, Nyumba za Ufumu zinamangidwa ndipo apainiya apadera anatumizidwa kumene kunalibe Mboni zambiri.

Kuyambira mu 2002 mpaka 2013 (Gawo 2)

A Mboni za Yehova m’mayiko awiriwa akukhulupirira kuti anthu ambiri ayamba kuphunzira Baibulo.

Tinkafunitsitsa Kutumikira Yehova

Philip Tengbeh ndi mkazi wake anathawa kuti asaphedwe pamene zigawenga anabwera mumzinda wa Koindu kumene ankakhala. Iwo anathandiza kumanga Nyumba za Ufumu zokwana 5 pamene ankakhala m’makampu a anthu othawa kwawo.

Ndinayamba Kulikonda Kwambiri Dziko la Sierra Leone

Cindy McIntire wakhala akutumikira monga mmishonale ku Africa kuyambira mu 1992. Iye akufotokoza chifukwa chake amakonda kwambiri kulalikira ku Sierra Leone.

Zimene Zinachitika Zaka 100 Zapitazo—1914

1914, chaka chimene Ophunzira Baibulo ankachilengeza, tsopano chinafika.