Kodi Baibulo Ingatiphunzitse Ciani?

Cifuno ca buku ino ni kukuthandizani kuphunzila zimene Baibulo ikamba pa nkhani zosiyana-siyana monga cimene cipangitsa kuti tizivutika, cimene cimacitika munthu akafa, mokhalila na cimwemwe m’banja, na zina zambili.

Kodi Mulungu Ali Nafe Colinga Canji?

Mwina mungafunse kuti n’cifukwa ninji masiku ano kuli mavuto ambili conco. Baibulo imaphunzitsa kuti posacedwa Mulungu adzacotsa mavuto, matenda, na imfa pa dziko lapansi.

NKHANI 1

Kodi Mulungu N’ndani?

Kodi muganiza kuti Mulungu amasamala za inu? Phunzilani za mmene Mulungu alili ndi mmene mungakhalile bwenzi lake.

NKHANI 2

Baibulo ni Buku Yocokela kwa Mulungu

Kodi Baibulo ingakuthandizeni bwanji pa mavuto anu? N’cifukwa ciani muyenela kukhulupilila maulosi a m’Baibulo?

NKHANI 3

Kodi Cifunilo ca Mulungu kwa Anthu n’Ciani?

Dziko likadzakhala paladaiso, kodi umoyo udzakhala bwanji?

NKHANI 4

Kodi Yesu Khiristu N’ndani?

Dziŵani cifukwa cake Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa, kumene anacokela, ndi cifukwa cake ali Mwana wa Yehova wobadwa yekha.

NKHANI 5

Dipo Ndiyo Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse

Kodi dipo n’ciani? Nanga mufunika kucita ciani kuti mupindule nayo?

NKHANI 6

Munthu Akafa Amayenda Kuti?

Phunzilani m’Baibulo zimene zimacitika munthu akafa, ndi cimene anthu timafela

NKHANI 7

Akufa Adzauka!

Kodi kumanda kuli wokondedwa wanu aliyense? Kodi mudzamuonanso? Phunzilani zimene Baibulo imakamba za kuuka kwa akufa.

NKHANI 8

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Anthu ambili amalidziŵa Pemphelo la Ambuye. Kodi mau akuti: “Ufumu wanu ubwele,” amatanthauza ciani?

NKHANI 9

Kodi Mapeto a Dziko Ali Pafupi?

Zocita ndi makhalidwe a anthu m’dzikoli zionetselatu kuti mapeto a dziko lomba ali pafupi kweni-kweni, monga mmene Baibulo imakambila.

NKHANI 10

Kudziŵa Bwino za Angelo

Baibulo imatidziŵitsa bwino za angelo ndi ziŵanda. Kodi zolengedwa za mzimu zimenezi zilikodi? Kodi zingatithandize kapena kutivulaza?

NKHANI 11

N’Cifukwa Ciani pa Dziko Lapansi Pali Mavuto Ambili Conco?

Anthu ambili amaganiza kuti Mulungu ni amene amabweletsa mavuto. Nanga inu muganiza bwanji? Mulungu amatiuza cifukwa cake tivutika.

NKHANI 12

Zimene Mungacite Kuti Mukhale Bwenzi la Mulungu

Mungakhale ndi umoyo wokondweletsa Yehova. Zoona, mungakhale bwenzi lake.

NKHANI 13

Muzilemekeza Mphatso ya Moyo

Kodi Mulungu amaona bwanji kucotsa mimba, kuikidwa magazi, ndi moyo wa nyama?

NKHANI 14

Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe

Cikondi cimene Yesu anaonetsa ni citsanzo kwa amuna, akazi, makolo, ndi ana. Nanga tiphunzilapo ciani kwa iye?

NKHANI 15

Kulambila Mulungu Koyenela

Onani mfundo 6 zimene mungadziŵile amene amalambila m’njila ya Mulungu.

NKHANI 16

Sankhani Kulambila Mulungu

Ndi mavuto abwanji amene mungakumane nawo pouza anthu ena zimene mumakhulupilila? Mungacite bwanji kuti muziuzako ena zimene mumakhulupilila koma osakhumudwitsa?

NKHANI 17

Mwayi wa Pepemphelo

Kodi Mulungu amamvela mukapemphela? Kuti mupeze yankho pa funso limeneli, muyenela kudziŵa zimene Baibulo imaphunzitsa pa nkhani ya pemphelo.

NKHANI 18

Kodi Nidzipeleke kwa Mulungu ndi Kubatizika?

Ni masitepu ati ofunika kuti munthu abatizike? Phunzilani zimene ubatizo umatanthauza ndi mmene uyenela kucitikila.

NKHANI 19

Khalani Pafupi ndi Yehova

Tingaonetse bwanji kuti timamukonda Yehova ndi kuyamikila zonse zimene amaticitila?

Zakumapeto

Tanthauzo la mau ali m’buku yakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse