Onani zimene zilipo

Mavidiyo Othandiza Kumvetsa Mfundo Zofunika za m’Baibo

Mavidiyo amenewa ali na mayankho a mafunso ofunika kwambili a m’Baibo, monga akuti: N’cifukwa ciyani Mulungu analenga dziko lapansi? Kodi Akufa Ali mu Mkhalidwe Wabwanji? komanso N’cifukwa Ciyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

Kodi Kumwamba na Dziko Lapansi Zinacita Kulengedwa?

Anthu ambili samvetsetsa zimene Baibo imakamba ponena za cilengedwe, ndipo ena amati ni nthano cabe. Kodi zimene Baibo imakamba n’zoona?

Kodi Mulungu Alikodi?

Umboni woonetsa kuti Mulungu alikodi ni womveka.

Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?

Mulungu ali na maina audindo ambili monga Wamphamvuyonse, Mlengi, ndi Ambuye. Koma dzina la Mulungu lipezeka m’Baibulo nthawi zoposa 7,000.

Ndani Analemba Baibulo?

Ngati anthu na amene analemba Baibulo, kodi ingachedwe Mau a Mulungu? Kodi m’Baibulo muli maganizo a ndani?

Tingatsimikizile Bwanji Kuti Baibulo Limakamba Zoona?

Ngati Mlembi wa Baibulo ni Mulungu, ndiye kuti iyenela kukhala yosiyana na mabuku ena onse.

Kodi Colinga ca Moyo N’ciyani?

Dziŵani mmene mungakhalile na cimwemwe ceniceni komanso moyo waphindu.

Kodi Mungawapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili pa Umoyo?

Kodi muli na mafunso okhudza moyo, imfa, kapena tsogolo? Mayankho okhutilitsa a mafunso amenewa komanso ena amapezeka. Kodi amapezeka kuti?

Kodi Akufa Ali mu Mkhalidwe Wabwanji?

Baibo imalonjeza kuti kutsogoloku, anthu ambili-mbili adzaukitsidwa, monga mmene zinacitila kwa Lazaro.

Kodi Yesu Khristu ni Mulungu?

Kodi Yesu Khristu ndiye Mulungu Wamphamvuzonse? Kapena ni osiyana?

N’cifukwa Ciani Yesu Anafa?

Baibo imaonetsa kuti imfa ya Yesu ni yofunika kwambili. Kodi imfa yake inali na colinga canji?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Pa utumiki wake wonse, Yesu anaphunzitsa kwambili za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Otsatila ake akhala akupemphela kuti Ufumuwo ubwele kwa zaka zambili.

Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulila mu 1914

Zaka zoposa 2,600 zapitazo, Mulungu anacititsa mfumu inayake yamphamvu kulota maloto aulosi. Ulosi umenewo ukukwanilitsidwa masiku ano.

Dziko Linasintha Kuyambila mu 1914

Zocitika na makhalidwe a anthu padzikoli kuyambila mu 1914 zimaonetsa kuti maulosi a m’Baibo okamba za ”masiku otsiliza” akukwanilitsidwa.

Kodi Mulungu Ndiye Amacititsa Matsoka a Zacilengedwe?

Anthu aŵili amene anakumanapo na matsoka a zacilengedwe akufotokoza zimene anaphunzila m’Baibo.

Kodi Mulungu Amavomeleza Zifanizilo Pomulambila?

Kodi angatithandize kuyandikila Mulungu amene sitingamuone?

Kodi Mulungu Amauona Bwanji Ukwati?

Mulungu amafuna kuti ukwati wanu ukhale wopambana. Malangizo abwino a m’Baibo athandiza anthu ambili okwatilana.

Kodi Kuonelela Zamalisece N’kucimwila Mulungu?

Kodi liwu lakuti “zamalisece” lilimo m’Baibo? Kodi tingadziŵe bwanji mmene Mulungu amaonela nkhani yoonelela zamalisece?