Ufumu wa Mulungu Ukulamulila

Anthu ofika m’mamiliyoni akhala ndi moyo wacimwemwe komanso wotetezeka m’boma la Mulungu labwino. Kodi mungakonde kukhala nzika ya bomalo?

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kodi cilengezo colimbikitsa cimene m’bale C. T. Russell anapeleka pa October 2, 1914 cakwanilitsika bwanji?

NKHANI 1

“Ufumu Wanu Ubwele”

Yesu anali kukonda kuphunzitsa za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Kodi udzacita ciani ukadzabwela, ndipo udzabwela liti?

NKHANI 2

Ufumu Wabadwa Kumwamba

Kodi ndani anathandiza anthu a Kristu kukonzekela Ufumu? Kodi ndi zinthu ziti zimene zimaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma leni-leni?

NKHANI 3

Yehova Anaulula Colinga Cake

Kodi Ufumu wa Mesiya unali mbali ya colinga ca Yehova kucokela paciyambi? Kodi Yesu anamveketsa bwanji coonadi conena za Ufumu wa Mulungu?

NKHANI 4

Yehova Akweza Dzina Lake

Kodi Ufumu wa Mulungu wacita zotani pofuna kuyeletsa dzina la Mulungu? Kodi inuyo mungathandize bwanji kuyeletsa dzina la Yehova?

NKHANI 5

Mfumu Imveketsa Bwino Mfundo Zokhudza Ufumu wa Mulungu

Phunzilani kuti mudziŵe bwino Ufumu wa Mulungu, olamulila ake, nzika zake ndi zimene mungacite kuti mukhale okhulupilika ku ufumuwo.

NKHANI 6

Anthu Amene Amalalikila—Atumiki Akudzipeleka Mofunitsitsa

N’cifukwa ciani Yesu anali ndi cidalilo cakuti adzakhala ndi atumiki odzipeleka m’masiku otsiliza? Nanga mungaonetse bwanji kuti mumaika Ufumuwo patsogolo pa moyo wanu?

NKHANI 7

Njila Zolalikilila—Kugwilitsila Nchito Njila Zosiyanasiyana Polalikila Anthu

Onani njila zamakono zimene anthu a Mulungu akhala akugwilitsila nchito kuti alengeze uthenga wabwino kwa anthu ambili mmene angathele mapeto asanafike.

NKHANI 8

Zida Zogwilitsila Nchito Polalikila—Kusindikiza Mabuku Ogaŵila Padziko Lonse Lapansi

Kodi nchito yathu yomasulila imapeleka bwanji umboni wakuti Yesu akucilikiza nchitoyi? Mukaganizila zofalitsa zathu, n’ciani cimakupangitsani kukhulupilila kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni?

NKHANI 9

Zotsatilapo za Nchito Yolalikila—“M’Mindamo, Mwayela Kale ndipo m’Mofunika Kukolola”

Yesu anaphunzitsa otsatila ake mfundo ziŵili zofunika kwambili zokhudza nchito yokolola mwa kuuzimu. Kodi mfundozo zikutikhudza motani masiku ano?

NKHANI 10

Mfumu Iyenga Anthu Ake Mwakuuzimu

Kodi Krisimasi ndi mtanda zimafanana bwanji?

NKHANI 11

Kuyenga Anthu a Mulungu Mwamakhalidwe—Kuonetsa Ciyelo ca Mulungu

Zipinda za alonda ndiponso zipata za kacisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya, zakhala ndi tanthauzo lapadela kwa anthu a Mulungu kuyambila mu 1914.

NKHANI 12

Gulu Lotumikila “Mulungu Wamtendele”

N’cifukwa ciani Baibulo limasiyanitsa khalidwe lacisokonezo ndi khalidwe lamtendele? Nanga yankho la funso limeneli limakhudza bwanji Akristu masiku ano?

NKHANI 13

Alaliki a Ufumu Amapeleka Milandu Yao ku Khoti

Masiku ano, oweluza ena ku makhoti akuluakulu amaweluza ngati Gamaliyeli, mphunzitsi wakale wa Cilamulo.

NKHANI 14

Kucilikiza Boma la Mulungu Mokhulupilika

“Mtsinje” wa cizunzo umene Mboni za Yehova zakumana nao cifukwa cokana kutenga mbali m’zandale wamezedwa ndi anthu osayembekezeka.

NKHANI 15

Kumenyela Ufulu wa Kulambila

Anthu a Mulungu akhala akumenyela ufulu wao womvela malamulo a Ufumu wa Mulungu.

NKHANI 16

Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu

Kodi tingacite ciani kuti tipindule mokwanila ndi misonkhano imene timakhala nayo kuti tilambile Yehova?

NKHANI 17

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

Kodi masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu athandiza bwanji atumiki a Ufumu kukwanilitsa utumiki wao?

NKHANI 18

Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito Za Ufumu

Kodi ndalama zimacokela kuti? Nanga zimagwila nchito yanji?

NKHANI 19

Nchito Yomanga Imene Imalemekeza Yehova

Malo olambilila amalemekeza Mulungu. Koma pali cinthu cina cimene iye amaona kuti n’cofunika kwambili.

NKHANI 20

Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

Timadziŵa bwanji kuti nchito yopeleka thandizo pakacitika ngozi ndi mbali ya utumiki wathu wopatulika kwa Yehova?

NKHANI 21

Ufumu wa Mulungu Udzaononga Adani Ake

Muyenela kukonzekela tsopano kaamba ka nkhondo ya Aramagedo.

NKHANI 22

Ufumu Ukwanilitsa Cifunilo ca Mulungu Padziko Lapansi

Kodi mungatsimikize bwanji kuti zimene Yehova analonjeza zidzakwanilitsidwa?