Mavidiyo Ofotokoza Mabuku a m’Baibo

Mfundo zacidule zokhudza buku lililonse la m’Baibo.

Mfundo Zokhudza Buku la Ekisodo

Mulungu anatulutsa Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo na kuwapanga kukhala mtundu wodzipatulila kwa iye.

Mfundo Zokhudza Buku la Levitiko

Onani mmene buku la Levitiko limafotokozela ciyelo ca Mulungu komanso cifukwa cake kukhala woyela n’kofunika kwambili kwa ife.

Mfundo Zokhudza Buku la Numeri

Onani cifukwa cake kumvela Yehova pa zocitika zilizonse n’kofunika kwambili komanso cifukwa cake tiyenela kulemekeza anthu amene iye waaika kukhala otsogolela.

Mfundo Zokhudza Buku la Yoswa

Onani mmene mtundu wa Aisiraeli unagonjetsela dziko limene Mulungu anawapatsa, na mmene analigaŵila.

Mfundo Zokhudza Buku la Oweruza

Bukuli limafotokoza zocitika zambili, ndipo linatenga dzina lake kucokela kwa amuna olimba mtima acikhulupililo amene Mulungu anawaseŵenzetsa populumutsa Aisiraeli kwa anthu owapondeleza.

Mfundo Zokhudza Buku la Rute

Buku la Rute limakamba za cikondi codzimana cimene mkazi wina wamasiye anaonetsa apongozi ake aakazi, amenenso anali amasiye. Limakambanso mmene Yehova anadalitsila akazi awiliwa.

Mfundo Zokhudza Buku la 1 Mafumu

Onani mmene zinthu zinalili kuyambila pamene Aisiraeli anali paulemelelo mu ufumu wa Solomo mpaka m’nthawi ya mavuto mu ufumu wa Isiraeli komanso Yuda.

Mfundo Zokhudza Buku la 2 Mafumu

Onani mmene kulambila mafano kunaipitsila ufumu wa kumpoto wa Isiraeli, komanso mmene Yehova anadalitsila anthu ocepa amene anali kum’lambila na mtima wathunthu.

Mfundo Zokhudza Buku la 1 Mbiri

Onani mzele wa makolo a mfumu yoopa Mulungu, Davide. Mvetselaninso mbili ya umoyo wake kucokela pamene anayikidwa kukhala mfumu ya Isiraeli mpaka pamene anamwalila.

Mfundo Zokhudza Buku la 2 Mbiri

Onani mmene mbili iyi ya mafumu a Yuda ionetsela kufunika kokhala wokhulupilika kwa Mulungu.

Mfundo Zokhudza Buku la Ezara

Yehova anasunga lonjezo lake lakuti adzamasula anthu ake ku ukapolo ku Babulo na kubwezeletsa kulambila koona ku Yerusalemu.

Mfundo Zokhudza Buku la Nehemiya

Buku la Nehemiya lili na maphunzilo ofunika kwambili kwa olambila oona masiku ano.

Mfundo Zokhudza Buku la Esitere

Zocitika za m’nthawi ya Esitere zimatithandiza kukhala na cikhulupililo cakuti Yehova Mulungu ali na mphamvu zopulumutsa anthu ake akakhala pa mayeselo masiku ano

Mfundo Zokhudza Buku la Yobu

Onse okonda Yehova adzayesedwa. Nkhani ya Yobu itipangitsa kukhala na cidalilo cakuti tingakwanitse kukhalabe okhulupilika komanso kucilikiza ucifumu wa Yehova.

Mfundo Zokhudza Buku la Masalimo

Masalimo amacilikiza ucifumu wa Yehova, amathandiza na kutonthoza anthu okonda Mulungu, komanso amaonetsa mmene dziko lidzasinthila kupitila mu Ufumu wake.

Mfundo Zokhudza Buku la Miyambo

Pezani malangizo a Mulungu pa mbali zonse za umoyo wanu, pa za nchito ngakhalenso za m’banja.

Mfundo Zokhudza Buku la Mlaliki

Mfumu Solomo anafotokoza zinthu zimene n’zofunikadi mu umoyo, ndipo anazisiyanitsa na zinthu zosemphana na nzelu ya umulungu.

Mfundo Zokhudza Buku la Nyimbo ya Solomo

Cikondi cosatha ca mtsikana wacisulami kwa m’busa wacinyamata cikufotokozedwa kuti “lawi la Ya.” Cifukwa ciani?

Mfundo Zokhudza Buku la Yesaya

Buku la Yesaya lili na maulosi amene amatithandiza kukhala na cidalilo cakuti Yehova ni Wokwanilitsa malonjezo ndiponso Mulungu wa cipulumutso.

Mfundo Zokhudza Buku la Yeremiya

Yeremiya anakhalabe wokhulupilika pa nchito imene Mulungu anam’patsa ngakhale kuti anakumana na mavuto. Ganizilani mmene citsanzo cake cingathandizile Akhristu masiku ano.

Mfundo Zokhudza Buku la Maliro

Yeremiya ndiye analemba bukuli; lionetsa cisoni cimene anthu anali naco Yerusalemu atawonongedwa. Lionetsanso mmene Mulungu amacitila cifundo anthu olapa

Mfundo Zokhudza Buku la Ezekieli

Modzicepetsa komanso molimba mtima, Ezekieli anakwanilitsa utumiki umene Mulungu anam’patsa olo kuti unali wovuta. Citsanzo cake n’colimbikitsa ngako kwa ise masiku ano.

Mfundo Zokhudza Buku la Danieli

DDanieli na anzake anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova pamayeselo onse amene anakumana nawo. Citsanzo cawo ndiponso kukwanilitsidwa kwa maulosi zingatilimbikitse m’nthawi ya mapeto ino.

Mfundo Zokhudza Buku la Hoseya

HUlosi wa Hoseya uli na maphunzilo ofunika kwa ise masiku ano. Maphunzilo okhudza cifundo ca Yehova kwa anthu olapa, na okhudza kulambila kumene Mulungu amafuna.

Mfundo Zokhudza Buku la Yoweli

buku la yoweli, mfundo, vidiyo, mneneli yoweli, tsiku la yehova, madalitso a ufumu, baibo, mavidiyo

Mfundo Zokhudza Buku la Amosi

Yehova anaseŵenzetsa munthu wodzicepetsa ameneyu kucita nchito yofunika. Tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cabwino ca Amosi?

Mfundo Zokhudza Buku la Obadiya

Ni buku lalifupi kwambili m‘Malemba a Ciheberi. Ulosiwu umatipatsa ciyembekezo na kutilonjeza za kukwezedwa kwa ucifumu wa Yehova.

Mfundo Zokhudza Buku la Yona

Mneneliyo analandila uphungu, anakwanilitsa utumiki wake, ndipo Mulungu anam’phunzitsa mfundo yofunika yokhudza cikondi cake cokhulupilika na cifundo. Zocitika zake zidzakukhudzani mtima.

Mfundo Zokhudza Buku la Mika

Ulosi wouzilidwa na Mulungu umenewu ungalimbitse cidalilo cathu cakuti Yehova amatipempha kucita zimene tingakwanitse komanso zotipindulitsa.

Mfundo Zokhudza Buku la Nahumu

Ulosiwu umatipatsa cidalilo cakuti nthawi zonse Yehova amakwanilitsa mau ake na kuti amatonthoza onse ofuna-funa mtendele na cipulumutso cake mu Ufumu wake.

Mfundo Zokhudza Buku la Habakuku

Tingakhale na cidalilo cakuti nthawi zonse Yehova amadziŵa bwino njila yoyenela komanso nthawi yopulumutsila anthu ake.

Mfundo Zokhudza Buku la Zefaniya

N’cifukwa ciani tifunika kupewa maganizo akuti tsiku la Yehova la ciweluzo silidzafika?

Mfundo Zokhudza Buku la Hagai

Ulosiwu uunikila ubwino woika kulambila Mulungu pamalo oyamba m’malo mwa zofuna zathu.

Mfundo Zokhudza Buku la Zekariya

Atumiki a Mulungu akale analimbikitsidwa na Masomphenya ouzilidwa komanso maulosi ambili. Maulosi amenewa amatitsimikizila kuti Yehova akuticilikiza masiku ano.

Mfundo Zokhudza Buku la Malaki

Ni ulosi umene umakamba za mfundo zosasintha za Yehova, cifundo, na cikondi cake. Ulosiwu umatiphunzitsanso zina zokhudzana na zimene timakumana nazo masiku ano.

Mfundo Zokhudza Buku la Mateyu

Phunzilani mfundo zina zokhudza buku la m’Baibo limeneli, loyamba pa Mauthenga Abwino anayi.

Mfundo Zokhudza Buku la Maliko

Ni buku lalifupi kwambili pa Mauthenga Abwino. Buku la Maliko limatipatsa cithunzi ca mmene ulamulilo wa Yesu monga mfumu ya Ufumu wa Mulungu udzakhalila m’tsogolo.

Mfundo Zokhudza Buku la Luka

Ni nkhani ziti mu Uthenga Wabwino wa Luka zimeme m’mabuku ena a Uthenga wabwino mulibe?

Mfundo Zokhudza Buku la Yohane

Buku la Yohane lifotokoza za cikondi ca Yesu pa anthu, citsanzo cake ca kudzicepetsa, na zimene zinamudziŵikitsa kuti ni Mesiya​—Mfumu ya m’tsogolo ya Ufumu wa Mulungu.

Mfundo Zokhudza Buku la Machitidwe a Atumwi

Akhristu oyambilila anagwila nchito mwakhama kuti apange ophunzila m’mitundu yonse ya anthu. Buku la Machitidwe lingakuthandizeni kukhala acangu komanso akhama kwambili mu ulaliki.

Mfundo Zokhudza Buku la Aroma

Malangizo ouzilidwa okamba za kupanda tsankho kwa Yehova, ndiponso kufunika kokhala na cikhulupililo mwa Yesu Khristu.

Mfundo Zokhudza Buku la Akorinto Woyamba

M’kalata ya Paulo, muli malangizo ouzilidwa okamba za mgwilizano, makhalidwe oyela, cikondi, komanso ciyembekezo cakuti akufa adzauka.

Mfundo Zokhudza Buku la 2 Akorinto

Yehova, “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse,” amalimbitsa atumiki ake na kuwathandiza.

Mfundo Zokhudza Buku la Agalatiya

Kalata ya Paulo kwa Agalatiya ni yothandizanso masiku ano monga mmene zinalili pamene inalembedwa. Imathandiza Akhristu onse oona kukhalabe okhulupilika.

Mfundo Zokhudza Buku la Aefeso

Kalata youzilidwa imeneyi ifotokoza colinga ca Mulungu codzabweletsa mtendele na mgwilizano kupitila mwa Yesu Khristu.

Mfundo Zokhudza Buku la Afilipi

Tikakhala olimba pokumana na mayeselo, timalimbikitsa ena kuti asabwelele m’mbuyo.

Mfundo Zokhudza Buku la Akolose

Tingakondweletse Yehova mwa kuseŵenzetsa zimene timaphunzila, mwa kukhululukilana na mtima wonse, ndiponso mwa kuzindikila udindo wa Yesu na ulamulilo wake.

Mfundo Zokhudza Buku la 1 Atesalonika

Tifunika kukhala ogalamuka mwauzimu, ‘kutsimikizila zinthu zonse,’ ‘kupemphela mosalekeza,’ ndiponso kulimbikitsana.

Mfundo Zokhudza Buku la 2 Atesalonika

Paulo anawongolela maganizo olakwika a anthu ponena zakubwela kwa tsiku la Yehova, ndipo analimbikitsa abale kukhalabe olimba m’cikhulupililo.

Mfundo Zokhudza Buku la 1 Timoteyo

Paulo analemba 1 Timoteyo pofuna kufotokoza mmene zinthu ziziyendela mu mpingo, kucenjeza za ziphunzitso zonama, komanso za kukonda ndalama.

Mfundo Zokhudza Buku la 2 Timoteyo

Paulo analimbikitsa Timoteyo kukwanilitsa mbali zonse za utumiki.

Mfundo Zokhudza Buku la Tito

Kalata ya Paulo kwa Tito, inakamba za mavuto amene anali ku mipingo ya ku Kerete. Inakambanso za ziyenelezo za akulu.

Mfundo Zokhudza Buku la Filimoni

Kalata yacidule koma yamphamvu imeneyi ili na malangizo othandiza pankhani ya kudzicepetsa, kukoma mtima, na kukhululuka.

Mfundo Zokhudza Buku la Aheberi

Kulambila kwa cikhristu kumazikidwa pa zinthu zapamwamba kuposa akacisi na nsembe za nyama.

Mfundo Zokhudza Buku la Yakobo

Pophunzitsa mfundo zofunika zacikhristu, Yakobo anaseŵenzetsa mafanizo ambili ocititsa cidwi.

Mfundo Zokhudza Buku la 1 Petulo

Kalata yoyamba ya Petulo imatilimbikitsa kukhala ogalamuka komanso kutulila Mulungu nkhawa zathu zonse.

Mfundo Zokhudza Buku la 2 Petulo

Kalata yaciŵili ya Petulo, imatilimbikitsa kukhala okhulupilika pamene tiyembekezela kumwamba kwatsopano na dziko lapansi latsopano.

Mfundo Zokhudza Buku la 2 Yohane

Kalata yaciŵili ya Yohane itikumbutsa kuti tifunika kupitiliza kuyenda m’coonadi ndiponso kudziteteza kwa anthu onyenga.

Mfundo zokhudza buku la 3 Yohane

Kalata yacitatu ya Yohane itiphunzitsa mfundo yabwino yakuti tizikhala oceleza monga Akhristu.

Mfundo zokhudza buku la Yuda

Yuda anavumbula njila za anthu oipa amene anafuna kusoceletsa mpingo Wacikhristu na kuuwononga.

Mfundo Zokhudza Buku la Chivumbulutso

Masomphenya ocititsa cidwi a m’buku la Chivumbulutso aonetsa mmene Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsila cifunilo ca Mulungu kwa anthu pa dziko lapansi.