Phunzitsani Ana Anu

Makolo, gwilitsilani nchito nkhani zimenezi pophunzitsa ana anu.

Mau Oyamba

Mau a m’buku la Deuteronomo angakutsogoleleni ndi kukuthandizani pamene mukulela ana anu.

Cisinsi Cimene Ndife Okondwela Kudziŵa

Baibulo limakamba za cisinsi capadela kwambili ndipo cimachedwa “cisinsi copatulika.” Kodi ungakonde kucidziŵa?

PHUNZILO 2

Rabeka Anafuna Kukondweletsa Yehova

Kodi tingacite ciani kuti tikhale monga Rabeka? Ŵelenga nkhani yake kuti uphunzile zambili za iye.

PHUNZILO 3

Rahabi Anakhulupilila Yehova

Ŵelenga mmene Rahabi ndi banja lake anapulumutsidwila pamene Yeriko anaonongedwa.

PHUNZILO 4

Anakondweletsa Atate Wake ndi Yehova

Kodi mwana wa Yefita anasunga lonjezo liti? Kodi tingatsanzile bwanji citsanzo cake?

PHUNZILO 5

Samueli Sanaleke Kucita Zabwino

Kodi ungatsanzile bwanji citsanzo ca Samueli ndi kupitiliza kucita zabwino ngakhale kuti anthu ena akucita zoipa?

PHUNZILO 6

Davide Sanacite Mantha

Ŵelenga nkhani imeneyi m’Baibulo kuti udziŵe zimene zinacititsa Davide kukhala wolimba mtima.

PHUNZILO 7

Kodi Nthawi Zina Umaona kuti Uli Wekha Ndipo Ukucita Mantha?

Kodi Yehova anamuuza ciani Eliya pamene anali yekha? Kodi uphunzilapo ciani pa zimene zinacitikila Eliya?

PHUNZILO 8

Yosiya Anali ndi Anzake Abwino

Baibulo limatiuza kuti mnyamata wina dzina lake Yosiya anali kuvutika kwambili kucita zabwino. Phunzila kuti udziŵe mmene anzake anamuthandizila.

PHUNZILO 9

Yeremiya Sanaleke Kulankhula za Yehova

Ngakhale kuti anthu anali kumunyoza ndi kumukalipila, n’cifukwa ciani Yeremiya sanaleke kulankhula za Mulungu?

PHUNZILO 10

Nthawi Zonse Yesu Anali Womvela

Nthawi zina kumvela makolo ndi kovuta. Phunzila mmene citsanzo ca Yesu cingakuthandizile.

PHUNZILO 11

Analemba za Yesu

Phunzila za anthu 8 amene analembako Baibulo amene anakhalapo ndi moyo panthawi imodzi ndi Yesu ndipo analemba za moyo wake.

PHUNZILO 12

Mwana wa Mlongo wa Paulo Anali Wolimba Mtima

Mnyamata ameneyu anapulumutsa amalume ake. Kodi iye anacita ciani?

PHUNZILO 13

Timoteyo Anafunitsitsa Kuthandiza Anthu

Kodi n’ciani cingakuthandize kukhala ndi umoyo wabwino ndi wosangalatsa monga Timoteyo?

PHUNZILO 14

Ufumu Umene Udzalamulila Dziko Lonse

Kodi zinthu zidzakhala bwanji Yesu akadzayamba kulamulila dziko lapansi? Kodi ungakonde kuti udzakhalemo?