Kalata Yopita kwa Aheberi 2:1-18

  • Tiziganizira mozama kuposa nthawi zonse (1-4)

  • Zonse zinaikidwa pansi pa mapazi a Yesu (5-9)

  • Yesu ndiponso abale ake (10-18)

    • Mtumiki Wamkulu wa chipulumutso (10)

    • Mkulu wa ansembe wachifundo (17)

2  Nʼchifukwa chake zinthu zimene tinamva tiyenera kuziganizira mozama kuposa nthawi zonse,+ kuti tisatengeke pangʼonopangʼono nʼkusiya chikhulupiriro.+  Chifukwa ngati mawu amene angelo ananena+ analidi oona, ndipo chilango chinaperekedwa mwachilungamo pa tchimo lililonse ndi kusamvera kulikonse,+  ndiye tidzapulumuka bwanji ngati titanyalanyaza chipulumutso chachikulu chonchi?+ Ambuye wathu ndi amene anayamba kunena za chipulumutsochi+ ndipo anthu amene anamumva anatitsimikizira zimenezo.  Mulungu nayenso anachitira umboni za chipulumutsochi pogwiritsa ntchito zizindikiro, zinthu zodabwitsa, ntchito zamphamvu zosiyanasiyana+ komanso mzimu woyera umene anaupereka mogwirizana ndi chifuniro chake.+  Dziko lapansi limene likubweralo, limene ife tikunena, sanaliike pansi pa ulamuliro wa angelo.+  Koma mboni ina inanena penapake kuti: “Munthu ndi ndani kuti muzimuganizira, kapena mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimusamalira?+  Munamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo. Munamuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu ndipo munamuika kuti azilamulira ntchito za manja anu.  Mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Popeza Mulungu anaika zinthu zonse pansi pa Mwana wake,+ ndiye kuti palibe chilichonse chimene anasiya osachiika pansi pa Mwanayo.+ Komabe, panopa sitikuona kuti zinthu zonse zili pansi pake.+  Koma tikuona Yesu, amene anamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo.+ Panopa amuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anafa.+ Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, zimenezi zinamuchitikira kuti alawe imfa mʼmalo mwa munthu aliyense.+ 10  Zinthu zonse zinakhalapo kuti zipereke ulemerero kwa Mulungu komanso zinakhalapo kudzera mwa iye. Choncho kuti athandize ana ambiri kukhala ndi ulemerero,+ zinali zoyenera kuti achititse Mtumiki Wamkulu wachipulumutso chawo+ kukhala wangwiro kudzera mʼmavuto amene anakumana nawo.+ 11  Chifukwa onse, woyeretsa ndi amene ayeretsedwawo,+ amachokera kwa mmodzi.+ Choncho iye sachita manyazi kuwatchula kuti “abale” ake,+ 12  pamene akunena kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani poimba nyimbo pakati pa mpingo.”+ 13  Komanso pamene akunena kuti: “Ine ndidzamudalira.”+ Ndiponso kuti: “Taonani! Ine ndi ana amene Yehova* wandipatsa.”+ 14  Popeza “ana” onsewo ndi a magazi ndi mnofu, iyenso anakhala wa magazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake, awononge Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+ 15  Anachitanso zimenezi kuti amasule onse amene anali mu ukapolo moyo wawo wonse chifukwa choopa imfa.+ 16  Chifukwa sikuti iye akuthandiza angelo, koma akuthandiza mbadwa* za Abulahamu.+ 17  Choncho iye anayenera kukhala ngati “abale” ake pa zinthu zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo komanso wokhulupirika pa zinthu zokhudza Mulungu, nʼcholinga choti apereke nsembe yophimba machimo a anthu+ kuti tigwirizanenso ndi Mulungu. 18  Popeza iye anavutika pamene ankayesedwa,+ amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”