Wolembedwa ndi Mateyu 2:1-23

  • Okhulupirira nyenyezi anapita kukamuona (1-12)

  • Anathawira ku Iguputo (13-15)

  • Herode anapha ana aamuna (16-18)

  • Anabwerera ku Nazareti (19-23)

2  Yesu atabadwa ku Betelehemu+ wa ku Yudeya, pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Herode,*+ okhulupirira nyenyezi ochokera Kumʼmawa anabwera ku Yerusalemu.  Iwo ananena kuti: “Kodi mfumu ya Ayuda+ imene yabadwa posachedwapa ili kuti? Chifukwa pamene tinali Kumʼmawa, tinaona nyenyezi yake ndipo tabwera kudzamugwadira.”  Mfumu Herode komanso anthu onse a mu Yerusalemu atamva zimenezi, anavutika mumtima.  Choncho Herode anasonkhanitsa ansembe aakulu ndi alembi onse a anthu, ndipo anawafunsa za kumene Khristu* adzabadwire.  Iwo anamuyankha kuti: “Adzabadwira ku Betelehemu+ wa ku Yudeya, chifukwa mneneri analemba zimenezi kuti:  ‘Iwe Betelehemu wamʼdziko la Yuda, si iwe mzinda waungʼono kwambiri kwa olamulira a Yuda, chifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulira amene azidzaweta anthu anga, Aisiraeli.’”+  Kenako Herode anaitanitsa mwachinsinsi okhulupirira nyenyezi aja ndipo atawafunsa mosamala, anadziwa nthawi yeniyeni imene nyenyeziyo inaonekera.  Ndiyeno powatumiza ku Betelehemu, iye anawauza kuti: “Pitani mukamufunefune mwanayo mosamala. Mukakamupeza mubwere kudzandidziwitsa kuti nanenso ndipite kukamugwadira.”  Atamva zimene mfumu inanena, anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali Kumʼmawa+ ija inawatsogolera mpaka inakaima pamwamba pa nyumba imene munali mwanayo. 10  Ataona kuti nyenyeziyo yaima, anasangalala kwambiri. 11  Atalowa mʼnyumbamo, anaona mwana uja ndi mayi ake Mariya ndipo anagwada nʼkumuweramira. Kenako anatulutsa chuma chawo nʼkupereka kwa mwanayo golide, lubani ndi mule monga mphatso. 12  Koma chifukwa chakuti Mulungu anawachenjeza kudzera mʼmaloto+ kuti asapitenso kwa Herode, iwo anabwerera kudziko lakwawo kudzera njira ina. 13  Okhulupirira nyenyezi aja atachoka, mngelo wa Yehova* anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto+ nʼkumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo. Ukakhale kumeneko kufikira nthawi imene ndidzakuuze, chifukwa Herode akufuna kuyamba kufunafuna mwanayu kuti amuphe.” 14  Choncho Yosefe anadzuka usiku womwewo nʼkutenga mwana uja ndi mayi ake ndipo anachoka kumeneko nʼkupita ku Iguputo. 15  Iye anakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Zimenezi zinakwaniritsa zimene Yehova* ananena kudzera mwa mneneri wake kuti: “Ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.”+ 16  Ndiyeno Herode ataona kuti okhulupirira nyenyezi aja amupusitsa, anakwiya koopsa. Choncho anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna mʼBetelehemu ndi mʼzigawo zake zonse, kuyambira azaka ziwiri kutsika mʼmunsi. Anasankha kupha ana a zaka zimenezi mogwirizana ndi zimene okhulupirira nyenyezi aja anamuuza.+ 17  Zimenezi zinakwaniritsa mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya kuti: 18  “Mawu anamveka ku Rama. Kunamveka kulira mofuula ndiponso momvetsa chisoni. Anali Rakele+ amene ankalirira ana ake ndipo sanamve kutonthozedwa, chifukwa ana akewo kunalibenso.”+ 19  Herode atamwalira, mngelo wa Yehova* anaonekera mʼmaloto+ kwa Yosefe ku Iguputo 20  ndipo anamuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo upite mʼdziko la Isiraeli, chifukwa amene ankafuna kupha mwanayu* anamwalira.” 21  Choncho Yosefe ananyamuka nʼkutenga mwanayo ndi mayi ake nʼkukalowa mʼdziko la Isiraeli. 22  Koma atamva kuti Arikelao ndi amene akulamulira mʼmalo mwa bambo ake Herode ku Yudeya, anachita mantha kupita kumeneko. Komanso chifukwa chakuti Mulungu anamuchenjeza mʼmaloto,+ iye anapita mʼdera la Galileya.+ 23  Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritse mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Kapena kuti, “amene ankafuna moyo wa mwanayu.”
Nʼkutheka kuti dzinali likuchokera ku mawu a Chiheberi omwe angamasuliridwe kuti “Mphukira.”